Tsiku lina, amai anatenga ziphaso.
One day, mama got a lot of fruit.
“Tipemphako ziphaso” Tinapempha. “Tizadya ziphaso usiku walelo” Anatelo amai.
“When can we have some fruit?” we ask.
“We will have the fruit tonight,” says mama.
M’bale wanga Tahim ndiozikonda. Alawa zonse ziphaso. Adya ziphaso zambiri.
My brother Rahim is greedy. He tastes all the fruit. He eats a lot of it.
“Onani zimene Rahim anachita!” Anakuwa m’bale wanga wamg’ono. “Rahim ndiwamakani ndi wozikonda” Ndinatelo.
“Look at what Rahim did!” shouts my little brother.
“Rahim is naughty and selfish,” I say.
Amai ndiokalipa chifukwa cha Rahim.
Mother is angry with Rahim.
Naifenso ndife okwiya chifukwa cha Rahim. Koma Rahim sapepesa.
We are also angry with Rahim. But Rahim is not sorry.
“Kodi simuzamupasa chilango?” Afunsa m’bale wamng’ono.
“Aren’t you going to punish Rahim?” asks little brother.
“Rahim, posachedwa apa, uzachita chisoni”, amuchenjeza amai.
“Rahim, soon you will be sorry,” warns mama.
Rahim wayamba kumvela kudwala.
Rahim starts to feel sick.
“M’mimba mwanga mwayamba kuwawa” awelewetsa Rahim.
“My tummy is so sore,” whispers Rahim.
Amai anadziwa kuti izi zizachitika. Chipaso chimupasa chilango Rahim!
Mama knew this would happen. The fruit is punishing Rahim!
Pambuye pake, Rahim apepesa kwa ife. “Sindizakhalanso wazikonda tele,” alonjeza. Ndipo timukhulupirira tonse.
Later, Rahim says sorry to us. “I will never be so greedy again,” he promises.
And we all believe him.