Back to stories list
Zama ndi wamphamvu
Zama is great!
Michael Oguttu
Vusi Malindi
Jessy Sakala
Christine Mwanza
The audio for this story is currently not available.
M’ngono wanga amacedwa kugona.Ndimauka m’mamawa cifukwa ndine wa ngwilo!
My little brother sleeps very late. I wake early, because I am great!
Ndine ndimatsegulako kuti dzuwa lilowe.
I am the one who lets in the sun.
“Ndiwe nthanda yanga,” amatelo amai kundiwuza.
“You’re my morning star,” says Ma.
Ndimadzisamba ndekha matsiku onse, sindifunanso thandidzo ai.
I wash myself, I don’t need any help.
Sindimaganiza zakuti madzi ndiyodzidzila, kapena sopo wa kamtambo wocapila dzobvala.
I can cope with cold water and blue smelly soap.
Amai amandikumbutsa kuti “osayiwala kutsuka mano.” Ndimawayanka kuti “Ine ai, sindingaiwale ai!”
Ma reminds, “Don’t forget teeth.” I reply, “Never, not me!”
Ndikamalidza kusamba, ndimapatsa moni agogo amuna ndi alongo awo atate anga.Ndimawafunila tsiku labwino.
After washing, I greet Grandpa and Auntie, and wish them a good day.
Ndipo ndimabvala ndekha.”Ndine wamkulu tsopano amama,” ndimawaudza.
Then I dress myself, “I’m big now Ma,” I say.
Ndimanga mabatani komanso nthambo za nsapato ndekha.
I can close my buttons and buckle my shoes.
Ndimayesetsa kuti mbale wanga adziwe nkhani zonse za kusukulu.
And I make sure little brother knows all the school news.
Ndimacita zonse zothekela munjira mukalasi.
In class I do my best in every way.
Ndimacita zabwino zonsezi tsiku ndi tsiku.Koma ndimakondetsetsa kusowela kwambili!
I do all these good things every day. But the thing I like most, is to play and play!
Written by: Michael Oguttu
Illustrated by: Vusi Malindi
Translated by: Jessy Sakala
Read by: Christine Mwanza