Tom wanyamula nswanda.
Tom carries a tray of ripe bananas.
Tom amapita ku msika kukagulisa nthochi.
Tom goes to the market to sell bananas.
Anthu pa msika agula ziphaso.
People at the market are buying fruit.
Koma palibe amene agula nthochi za Tom. Asankha kugula nthochi za azimai.
But no one is buying
Tom’s bananas.
They prefer to buy fruit from women.
“M’mudzi mwathu, azimai okha ndio amene agulitsa nthochi,” anthu amatelo. “Kodi uyu ndi mwamuna wotani?” Anthu afunsa.
“In our community, only women sell fruit,” people say. “What kind of a man is this?” people ask.
Koma Tom saleka. Apunda, ” Gulani nthochi zanga! Gulani nthochi zanga zakupsya komanso zonzuna.
But Tom does not give up.
He calls, “Buy my bananas!
Buy my sweet ripe bananas!”
Mkazi umozi atengapo nthochi zogula. Ayanganisisa nthochi mwachidwi.
One woman picks up a bunch of bananas from the tray.
She looks at the bananas carefully.
Mzimai agula nthochi.
The woman buys the bananas.
Anthu ambiri abwera kusitolo. Agula nthochi za Tom ndi kuzidya.
More people come to the stall.
They buy Tom’s bananas and eat them.
Posachedwa, zonse zatha. Tom awerengera ndalama zomwe wapanga.
Soon, the tray is empty.
Tom counts the money he earned.
Pambuyo pake, Tom agula sopo, shuga, ndi mkhate. Aika zinthu mu nswanda yake.
Then Tom buys soap, sugar, and bread.
He puts the things in his tray.
Tom waika nswanda yake pa mutu ndipo apita ku nyumba.
Tom balances the tray on his head and goes home.