Download PDF
Back to stories list

Andiswa kaswili wa masowera ampila Andiswa Soccer Star

Written by Eden Daniels

Illustrated by Eden Daniels

Translated by Sitwe Benson Mkandawire

Read by Christine Mwanza

Language Nyanja

Level Level 2

Narrate full story The audio for this story is currently not available.


Andiswa anawonelela anyamata kusowera mpila. Analakalaka kusowera nao. Anapempha asogoleli amasowera ngati angaloledwe kusowera nao.

Andiswa watched the boys play soccer. She wished that she could join them. She asked the coach if she can practise with them.


Asogoleli amasowera anaika manja yao muchiuno. “Pano pasukulu, anyamata okha ndiye ololedwa kusowera mpila,” anatero.

The coach put his hands on his hips. “At this school, only boys are allowed to play soccer,” he said.


Anyamata anamuuza kuti akasowere masowera ampila wam’manja. Ananena kuti mpila wam’manja ndi wa atsikana ndipo mpila wa mendo ndi wa anyamata. Andiswa anakhumudwa.

The boys told her to go play netball. They said that netball is for girls and soccer is for boys. Andiswa was upset.


Tsiku lotsatila, sukulu inakhala ndi masowera akulu ampila. Asogoleli ampila anadankhawa chifukwa kaswili wao wampila anadwala ndiponso sanakwanise kusewera mpila.

The next day, the school had a big soccer match. The coach was worried because his best player was sick and could not play.


Andiswa anathamagila kuli asogoleli amasowera ampila kupapata kuti amuvomeleze asowere. Musogoleli sanaziwe chochita. Anaganiza kuti Andiswa angasowere mpila.

Andiswa ran to the coach and begged him to let her to play. The coach was not sure what to do. Then he decided that Andiswa could join the team.


Masowera anali obvuta. Kulibe anagolesa kufika pakati panthawi.

The game was tough. Nobody had scored a goal by half time.


Munthawi yaciwiri yampila munyamata umodzi anapatsa Andiswa mpila. Musikana anayendesa kukagolesa. Anamenya mpila mwamphamvu nakugolesa kamozi.

During the second half of the match one of the boys passed the ball to Andiswa. She moved very fast towards the goal post. She kicked the ball hard and scored a goal.


Anthu otamba mpila anakondwela kwambiri. Kuchokera pa tsiku limenelo, atsikana analoledwa kusowera masowera ampila.

The crowd went wild with joy. Since that day, girls were also allowed to play soccer at the school.


Written by: Eden Daniels
Illustrated by: Eden Daniels
Translated by: Sitwe Benson Mkandawire
Read by: Christine Mwanza
Language: Nyanja
Level: Level 2
Source: Andiswa Soccer Star from African Storybook
Creative Commons License
This work is licensed under a Creative Commons Attribution-NonCommercial 3.0 International License.
Options
Back to stories list Download PDF