Download PDF
Back to stories list

Ana achikonga Children of wax

Written by Southern African Folktale

Illustrated by Wiehan de Jager

Translated by Sitwe Benson Mkandawire

Read by Christine Mwanza

Language Nyanja

Level Level 2

Narrate full story The audio for this story is currently not available.


Tsiku lina, kunali banja lina lokondwera.

Once upon a time, there lived a happy family.


Sanali kuyambana. Anali kuthandizila makolo ao panyumba ndi kumunda.

They never fought with each other. They helped their parents at home and in the fields.


Koma sanaloledwe kuyenda pafupi ndi moto.

But they were not allowed to go near a fire.


Anali kucita nchito iliyonse usiku. Cifukwa anapandidwa ndi chikonga (wax).

They had to do all their work during the night. Because they were made of wax!


Koma munyamata umodzi anali kufunisitsa kuyenda muzuwa.

But one of the boys longed to go out in the sunlight.


Tsiku lina, kufunisitsa kwake kunayenda pasogolo. Abale ace anamucenjeza…

One day the longing was too strong. His brothers warned him…


Koma anacedwa! Anasungunuka muzuwa lakupya kwambiri.

But it was too late! He melted in the hot sun.


Ana achikonga sanakondwele poona m’bale wao asungunika.

The wax children were so sad to see their brother melting away.


Koma anapangana zocita. Anapanga kanyoni kucoka ku cikonga ca m’bale wao.

But they made a plan. They shaped the lump of melted wax into a bird.


Anapeleka kanyoni m’bale wao pamwamba pa phiri.

They took their bird brother up to a high mountain.


Pamene zuwa linacoka, kanyoni kanambululuka nakuimba m’mamawa mu zuwa.

And as the sun rose, he flew away singing into the morning light.


Written by: Southern African Folktale
Illustrated by: Wiehan de Jager
Translated by: Sitwe Benson Mkandawire
Read by: Christine Mwanza
Language: Nyanja
Level: Level 2
Source: Children of wax from African Storybook
Creative Commons License
This work is licensed under a Creative Commons Attribution 3.0 International License.
Options
Back to stories list Download PDF