Schaltfläche PDF
Zurück zur Geschichteliste

Tsiku lamene ndinanyamukira panyumba kuyenda kumzinda Als ich mein Zuhause verließ und in die Stadt zog

Geschrieben von Lesley Koyi, Ursula Nafula

Illustriert von Brian Wambi

Übersetzt von Jones Jere Joshua

Gelesen von Christine Mwanza

Sprache Nyanja

Niveau Niveau 3

Vollständige Geschichte erzählen Zu dieser Geschichte ist noch kein Audio verfügbar.


Poimirira mabasi ag’ono kumudzi kwathu panali potanganidwa ndi mabasi olonga kwambiri. Pansi panalinso katundu oculuka ofunika kulongedwa. Oitanitsa anthuanali kufuula maina akumenemabasi amapita.

Der kleine Busbahnhof in meinem Dorf war voll mit Leuten und überladenen Bussen und auf dem Boden lag noch mehr Gepäck, das verladen werden musste. Händler riefen die Namen der Städte, wo ihre Busse hinfuhren.


“Taunu! Tauni! Kupita kumadzulo!” Ndinamvera oitanitsa kufuula. Iyo ndiyo basi ndimafuna kukwera.

„Stadt! Stadt! Richtung Westen!“ hörte ich einen Händler rufen. Diesen Bus musste ich nehmen.


Basi yakutauni inali pafupi kudzala,koma anthu ambirianali akali kukankha kuti alowe. Ena analonga katundu yao munsi mwa basi. Ena anaika moika katundu mkati mwa basi.

Der Bus in die Stadt war fast voll, aber mehr Menschen versuchten, noch einen Platz zu ergattern. Manche verstauten ihr Gepäck unter dem Bus, andere auf den Ablagen drinnen.


Okwera atsopano anagwira matikiti ao pomwe amafuna-funa pomwe angakhale mu basi yodzala ndi anthu. Azimai a ana ang’ono ang’ono anawakhazika bwino paulendo utali.

Neue Passagiere hielten ihr Ticket fest in der Hand, während sie nach einem Platz in dem vollen Bus suchten. Frauen mit kleinen Kindern bereiteten sie für die lange Reise vor.


Ndinaziika pafupi ndi dzenera. Munthu amena anakhala pafupi ndi ine anagwirira pulasitiki ya msipu. Anvala nkhwawilo zakale, khoti lakutha, ndipo amaoneka wamantha.

Ich quetschte mich an ein Fenster. Der Mann neben mir umklammerte seinen grünen Plastikbeutel. Er trug alte Sandalen und einen abgetragenen Mantel. Er sah nervös aus.


Ndinapenya kubwalo kwa basi ndipo ndinazindikira kuti ndinali kusiya mudzi wanga, kumalo komwe ndinakulira. Ndinali kupita ku tauni yaikulu.

Ich schaute nach draußen und mir wurde klar, dass ich dabei war, mein Dorf, den Ort, wo ich aufgewachsen war, zu verlassen. Ich war auf dem Weg in die große Stadt.


Kulonga kunamalizika ndipo aulendo onse anakhazikika pansi. Azamalonda naonso anali kuzipatikiza kulowa mubasi kugulitsa katundu wao ku aulendo. Aliyense anali kufuula maina azomwe zinalipo zogulitsa. Mau anamveka odabwitsa kwa ine.

Der Bus war fertig beladen und alle Passagiere saßen nun. Straßenverkäufer drängten sich immer noch in den Bus, um den Passagieren ihre Waren zu verkaufen. Sie alle riefen die Dinge aus, die sie anzubieten hatten. Die Wörter klangen so lustig für mich.


Aulendo ang’ono anagulako zakumwa, ane anagulako zakudya zotsekemera za zing’ono zing’ono ndipo anayamba kutamfuna. Aja amene analibe ndalama, monga ine tinangopenyerera.

Einige Passagiere kauften Getränke, andere kauften kleine Snacks und aßen. Die, die kein Geld hatten, so wie ich, sahen bloß zu.


Zocita zimenezi zinasokonezedwa ndi kulira kwa huta ya bus, kudziwitsa kuti tinali pafupi kunyamuka. Onenezera anafuulira ogulitsa kuti atuluke kubwalo.

Dieses Geschehen wurde vom Hupen des Busses unterbrochen, ein Zeichen, dass wir bereit für die Abfahrt waren. Der Händler rief den Straßenverkäufern zu auszusteigen.


Ogulitsa anakankhana wina ndi mnzace kuti atuluke mu basi. Ena anali kupereka cenji kwa apaulendo. Ena amayesa kugulitsa zinthu zao nthawi yothera.

Die Verkäufer schubsten sich gegenseitig, um nach draußen zu gelangen. Manche gaben Wechselgeld aus. Andere versuchten, noch schnell etwas zu verkaufen.


Pomwe basi imacoka pa sitesheni ya basi, ndinayangana padzenera. Ndinaganizira ngati ndizabweranso kumudzi wanga.

Als der Bus den Busbahnhof verließ, blickte ich aus dem Fenster. Ich fragte mich, ob ich jemals in mein Dorf zurückkommen würde.


Pomwe ulendo umacitika, mkati mwa basi munatentha kwambiri. Ndinatseka maso anga kuyesa kugona.

Je länger wir fuhren, desto wärmer wurde es im Bus. Ich schloss meine Augen und versuchte zu schlafen.


Koma maganizo anabwereanso kumudzi. Kodi amai anga adzakhala bwino? Kodi akalulu anga azabweretsa ndalama zirizonse? Kodi mukulu wanga adzakumbukira kuthirira mbeu zanga zamitengo?

Aber in Gedanken war ich noch zu Hause. Wird meine Mutter in Sicherheit sein? Werden meine Hasen Geld einbringen? Wird mein Bruder daran denken, meine Baumsetzlinge zu gießen?


Mnjira, ndinakumbukira dzina ya malo amene amalume anakhalako mu tauni yakulu. Ndinali ndikali kung’ung’udzira pamene tulo tunanigwira ndipo ndinagona.

Während der Fahrt prägte ich mir den Ort ein, wo mein Onkel in der großen Stadt wohnt. Ich murmelte ihn immer noch vor mich hin, als ich einschlief.


Maola asanundi anai atsatira, ndinauka ndi phokoso lalikulu ndi kuitana kwa apaulendo amubasi apita kumudzi kwanga. Ndinatenga cola canga cacing’ono ndi kulumphira kubwalo kwa basi.

Neun Stunden später wachte ich von lautem Gepolter und der Passagieransage für mein Dorf auf. Ich nahm meine kleine Tasche und sprang aus dem Bus.


Basi yobwerera kumudzi imadzala mofulumira. Mosacedwa inayamba ulendo wopita kum’mawa. Cofunikira ceni-ceni kwa ine tsopano, cinali cakuyamba kufuna-funa nyumba ya amalume anga.

Der Bus zurück ins Dorf füllte sich schnell. Bald würde er zurück Richtung Osten fahren. Das wichtigste für mich war es nun, das Haus meines Onkels zu finden.


Geschrieben von: Lesley Koyi, Ursula Nafula
Illustriert von: Brian Wambi
Übersetzt von: Jones Jere Joshua
Gelesen von: Christine Mwanza
Sprache: Nyanja
Niveau: Niveau 3
Quelle: The day I left home for the city aus African Storybook
Creative Commons Lizenz
Dieses Werk ist unter einer Creative Commons Namensnennung 4.0 Lizenz lizenziert.
Optionen
Zurück zur Geschichteliste Schaltfläche PDF