Matsiku amakedzana, anthu sanali kudziwa ciliconse. Sanadziwe kubzala mbeu, mwina kusoka zovala, mwina kupanga zitsulo zansimbi. Nyame mulungu wakumwamba anali ndi nzelu pa zonse zamdziko lapansi. Nzeluzi anazisungila bwino mu mbiya.
Hace mucho, mucho tiempo la gente no sabía nada. No sabían cómo cultivar, o cómo tejer tela, o cómo hacer herramientas de hierro. El dios Nyame arriba en el cielo tenía toda la sabiduría del mundo. La mantenía guardada en una vasija de barro.
Tsiku lina, Nyame anaganiza kupatsa Anansi mbiya ya nzelu. Nthawi iliyonse Anansi akayangana mumbiya, anaphunzilamo cinthu cina catsopano. Cinali cokondweletsa kwambili!
Un día, Nyame decidió darle la vasija de sabiduría a Anansi. Cada vez que Anansi se asomaba y miraba dentro de la vasija de barro, aprendía algo nuevo. ¡Qué impresionante!
Anansi waumbombo anaganiza, “Ndizaisunga bwino mbiya pamwamba pa mtengo wautali. Motelo izakhala yanga ndekha!” Anatenga nthambo yaitali, yakumangilila mbiya ndikuimangilila pamimba pake. Anayamba kukwela mtengo. Koma cinali cobvuta kukwela cifukwa mbiya inali kumugunda kumyendo nthawi yonse.
El codicioso Anansi pensó, “voy a guardar la vasija en la copa de un árbol muy alto. ¡Y será sólo mía!” Hiló un hilo largo, envolvió con él la vasija de barro, y lo ató a su cintura. Empezó a trepar el árbol. Pero se le hacía muy difícil trepar el árbol con la vasija constantemente pegándole en las rodillas.
Pamene zonsezi zinali kucitika, mwana mwamuna mung’ono wa Anansi anali imilile kuonelela pansi pacimtengo. Iye anati, “Kodi sicizakhala capafupi kukwela mtengo ngati mwamangilila mbiya kumusana?” Anansi anayesa kumangilila mbiya yodzala ndi nzelu kumusana ndipo iye anakwela mtengo mosabvutika.
Mientras tanto, el hijo pequeño de Anansi lo miraba desde abajo y le dijo, “¿No sería más fácil trepar si te ataras la vasija a tu espalda?” Anansi ató la vasija llena de sabiduría a su espalda y, efectivamente, fue mucho más fácil.
Posacedwa konse anafike pamwamba pa mtengo. Koma iye anaima naganiza, “Ine ndiyenela kukhala ndi nzelu zonse, koma apa mwana wanga ndiye anali ndi nzelu kupambanila ine!” Anansi anakalipa kwambili paizi motelo anataya mbiya ya nzelu pansi kucoka mucimtengo.
En un instante logró llegar a la copa del árbol. Pero entonces se detuvo a pensar: “Se supone que yo soy quien tiene toda la sabiduría, ¡pero mi hijo fue más listo que yo!” Anansi se enojó tanto que lanzó la vasija desde lo alto del árbol.
Mbiya inaphwanyika mtizidutswa itafika pansi. Pamenepo nzelu zinafalitsidwa kwa munthu aliyense. Ndiye mwamene anthu anaphunzilila kulima, kusoka zovala, kupanga zitsulo za nsimba ndi zinthu zina zimene anthu adziwa kucita.
Quedó hecha pedazos en el suelo. La sabiduría quedó libre y disponible para todos. Y así fue cómo la gente supo cultivar, tejer, hacer herramientas de hierro, y muchas otras cosas más.