Kale-kale nthawi ina, kunali banja lina lokondwera.
Es war einmal eine glückliche Familie.
Sanali kuyambana. Anali kuthandiza makolo ao panyumba ndi kumunda.
Sie stritten nie miteinander. Sie halfen ihren Eltern im Haus und auf den Feldern.
Koma sanaloredwe kupita pafupi ndi moto.
Aber sie durften nicht in die Nähe von Feuer.
Anali kucita nchito yonse usiku. Cifukwa anapandidwa ndi chikonga.
Sie mussten all ihre Arbeit nachts verrichten. Denn sie waren aus Wachs!
Koma mnyamata umodzi anali kufunitsitsa kuyenda mdzuwa.
Aber einer der Jungen sehnte sich nach dem Sonnenlicht.
Tsiku lina, kufunitsitsa kwake kunakula kwambiri. Abale ace anamucenjeza…
Eines Tages war die Sehnsucht zu groß. Seine Brüder warnten ihn …
Koma anacedwa! Anasungunuka mudzuwa lotentha kwambiri.
Aber es war zu spät! Er schmolz in der heißen Sonne.
Ana aphula sanakondwele poona m’bale wao asungunika.
Die Wachskinder waren sehr traurig sehen zu müssen, wie ihr Bruder dahin schmolz.
Koma anapangana zocita. Anaumba kambalame kucoka kuphula wa m’bale wao.
Aber sie schmiedeten einen Plan. Sie formten den geschmolzenen Wachsklumpen zu einem Vogel.
Anapereka m’bale wao mbalame pamwamba pa phiri.
Sie brachten ihren Vogelbruder auf einen hohen Berg.
Pamene dzuwa inakwera, kambalame kanauluka ndikuimba m’dzuwa ya m’mamawa.
Und als die Sonne aufging, flog er singend davon ins Morgenlicht.