Andiswa anapenyerera anyamata akusowera mpira. Analakalaka kusowera nao. Anapempha atsogoleri amasowera ngati angaloledwe kusowera nao.
Andiswa schaute den Jungen beim Fußballspielen zu. Sie wünschte, sie könnte auch in der Mannschaft sein. Sie fragte den Trainer, ob sie mit ihnen trainieren kann.
Atsogoleri amasowera anaika manja yao muciuno cake. “Pano pasukulu, anyamata okha ndiye ololedwa kusowera mpira,” anatero.
Der Trainer stemmte die Hände in die Hüften. „An dieser Schule dürfen nur Jungen Fußball spielen“, sagte er.
Anyamata anamuuza kuti akasowere masowera ampira wamanja. Ananena kuti irmpira wamanja ndi wa atsikana ndipo mpira wa miyendo ndi wa anyamata. Andiswa anakhumudwa.
Die Jungen sagten, sie solle Netzball spielen. Sie sagten, Netzball sei für Mädchen und Fußball für Jungs.
Tsiku lotsatira, sukulu inakhala ndi masowera akulu ampira. Asogoleri ampira anadankhawa cifukwa katswiri wao wampira anadwala ndiponso sanakwanitse kusewera mpira.
Am nächsten Tag gab es ein großes Fußballspiel. Der Trainer machte sich Sorgen, weil sein bester Spieler krank war und nicht spielen konnte.
Andiswa anathamagira kwa atsogoleri amasowera airmpira kupapata kuti amuvomeleze asowere. Musogoleli sanadziwe cocita. Anaganiza kuti Andiswa angasowere irmpira.
Andiswa lief zum Trainer und flehte ihn an, sie spielen zu lassen. Der Trainer wusste nicht, was er tun sollte. Dann beschloss er, Andiswa in die Mannschaft aufzunehmen.
Masowera anali obvuta. Kulibe anagoletsa kufika pakati panthawi yamasewera.
Das Spiel war hart. Zur Halbzeit hatte noch niemand ein Tor geschossen.
Munthawi yaciwiri yairmpira mnyamata m’modzi anapatsira Andiswa irmpira. Mtsikana anathamanga mwamsanga kupita kugolo . Anamenya mpira mwamphamvu ndikugoletsa cigoli.
Während der zweiten Halbzeit spielte einer der Jungen Andiswa den Ball zu. Sie bewegte sich sehr schnell auf das Tor zu. Sie schoss den Ball mit großer Wucht und erzielte ein Tor.
Anthu openyerera irmpira anakondwera kwambiri. Kucokera pa tsiku limenelo, atsikana analoledwa kusewera masowera airmpira pa sukuklu.
Die Zuschauer jubelten begeistert. Seit diesem Tag dürfen Mädchen an der Schule auch Fußball spielen.