Zurück zur Geschichteliste
Ganizo
Entscheidung
Ursula Nafula
Vusi Malindi
David Sani Mwanza
Christine Mwanza
Zu dieser Geschichte ist noch kein Audio verfügbar.
Mudzi wanga unali ndi mabvuto ambiri. Timaima m’mzere wautali umodzi kutunga madzi pa pompi imodzi.
In meinem Dorf gab es viele Probleme. Wir bildeten eine lange Schlange, um Wasser von einem Brunnen zu holen.
Tinayembekezera zakudya zoperekedwa ndi ena.
Wir warteten auf Essen, das für uns gespendet wurde.
Tinakhoma manyumba athu mwamsanga cifukwa coopa akawalala.
Wir verriegelten unsere Häuser früh gegen Diebe.
Ana ambiri analeka sukulu.
Viele Kinder gingen nicht mehr in die Schule.
Atsikana ang’ono ang’ono anasewenza maganyu m’midzi ina.
Junge Mädchen arbeiteten als Dienstmädchen in anderen Dörfern.
Anyamata ang’ono ang’ono anali kuyendayenda m’midzi ina ndipo ena anali kuchita ganyu m’minda ya ena.
Manche Jungen trieben sich im Dorf herum, während andere auf Höfen arbeiteten.
Pamene mphepo ikuntha, mapepala opanda nchito anapacikikairpa mitengo ndi mipanda.
Wenn der Wind blies, hingen Papierreste in den Bäumen und an Zäunen.
Anthu anacekedwa ndi magalasi oonongeka amane anataidwa mosasamala.
Leute schnitten sich an Glasscherben, die herumlagen.
Ndipo tsiku lina, pompi inauma ndipo migomo yathu inalibe madzi .
Eines Tages versiegte der Brunnen und unsere Wasserkanister blieben leer.
Atate anga anayenda khomo ndi khomo kupempha anthu kuti apite ku msonkhano wa m’mudzi.
Mein Vater ging von Haus zu Haus und lud die Leute zu einer Dorfversammlung ein.
Anthu anasonkhana pansi pa mtengo ukulu ndipo anamvesera.
Die Leute versammelten sich unter einem großen Baum und hörten zu.
Atate anga anaima nati, “Tifunika kusewenzera pamozi kuti tithetse mabvuto athu.”
Mein Vater stand auf und sagte: „Wir müssen zusammenarbeiten, um unsere Probleme zu lösen.“
Juma wa zaka zisanu ndi zitatu, omwe anakhala pa nthambi ya mtengo anakuwa nati “Ndingathandize ndi kusesa.”
Der achtjährige Juma rief von einem Baumstamm aus: „Ich kann beim Aufräumen helfen!“
Mai m’mozi anati “azimai angasewenze pamozi ndi ine kuti tirime zakudya.”
Eine Frau sagte: „Die Frauen können mit mir zusammen Essen anbauen.“
Bambo wina anaimirira nati “Amuna azakumba citsime.”
Noch ein Mann stand auf und erklärte: „Die Männer werden einen Brunnen graben.“
Tonse tinakuwa ndi mau amozi ndikuti, “tifunika kusintha myoyo yathu.” Kucoka pa tsiku lija, tinasewenzera pamozi kuthetsa mabvuto athu.
Wir alle riefen einstimmig: „Wir müssen unser Leben ändern.“ Von dort an arbeiteten wir zusammen, um unsere Probleme zu lösen.
Geschrieben von: Ursula Nafula
Illustriert von: Vusi Malindi
Übersetzt von: David Sani Mwanza
Gelesen von: Christine Mwanza