“Tauni! Tauni! Kupita kumadzulo!” Ndinamvela oitanitsa kufuula. Iyo ndiyo basi ndimafuna kukwela.
我听到售票员喊“进城啦!进城啦!往西去!”这就是我要乘坐的大巴车。
Basi yakutauni inali pafupi kudzala, koma anthu ambili anali akali kukankha kuti alowe. Ena analonga katundu yao munsi mwa basi. Ena anaika moika katundu mkati mwa basi.
Okwela atsopano anagwila matikiti ao pomwe amafuna-funa pomwe angakhale mu basi yodzala ndi anthu. Azimai a ana ang’ono ang’ono anawakhazika bwino paulendo utali.
刚上车的乘客们紧紧地抓着他们的车票,在拥挤的车厢里寻找座位,带着小孩的妇女们都坐得舒舒服服的。
Ndinaziika pafupi ndi dzenela. Munthu amena anakhala pafupi ndi ine anagwilila pulasitiki ya msipu. Anavala nkhwawilo zakale, khoti lakutha, ndipo amaoneka wamantha.
Mnjila, ndinakumbukila dzina ya malo amene amalume anakhalako mu mzinda ukulu. Ndinali ndikali kung’ung’udzila pamene tulo tunanigwila ndipo ndinagona.
在路上,我努力记住我叔叔在城市里的地址。我迷迷糊糊地说着地址,沉沉地睡去。
Maola asanu ndi anai atsatila, ndinauka ndi phokoso lalikulu ndi kuitana kwa apaulendo amubasi apita kumudzi kwanga. Ndinatenga cola canga cacing’ono ndi kulumphila kubwalo kwa basi.
过了九个小时,我被售票员的叫喊声吵醒了,他在喊乘客坐车回村庄。我一把抓住我的包,跳下了车。
Basi yobwelela kumudzi imadzala mofulumila. Mosacedwa inayamba ulendo wopita kum’mawa. Cofunikila ceni-ceni kwa ine tsopano, cinali cakuyamba kufuna-funa nyumba ya amalume anga.