下载 PDF
返回故事列表

Nyimbo ya Sakima 萨可满的歌声

作者 Ursula Nafula

插图 Peris Wachuka

译文 Sitwe Benson Mkandawire

配音 Christine Mwanza

语言 齐切瓦语

级别 3级

将整故事念出来 本故事尚未有语音版。


Sakima anali kukhala ndi makolo ake ndi mlongo wake wa zaka zakubadwa zinai. Anakhala pa malo a munthu wolemela, Nyumba yao inali ya uzu pothera pa mzere wa mitengo.

萨可满和他的父母,还有四岁的妹妹住在一起,他们住在一个富人的土地上,他们的茅草屋在一排大树的后面。


Pamene Sakima anali ndi zaka zitatu, anadwala ndipo anakhala wa khungu. Sakima anali ndi matalanta.

萨可满三岁的时候,生了一场大病,从此,萨可满就看不见了,其实萨可满是一个非常有天赋的孩子。


Sakima anali kukwanisa kuchita zinthu zambiri zomwe ana a zaka 6 sankakwanisa kuchita.Mwachisanzo, anali kukhala ndi anthu akalu a m’mudzi ndi kukamba zinthu zofunikira.

萨可满今年六岁,他会做很多同龄的男孩不会做的事情,比如,萨可满能和村里的老人坐在一起讨论重要的事情。


Makolo a Sakima anali kusewenza pa nyumba ya bambo wolemera. Anachoka panyumba m’mamawa ndi kubwelela kunyumba. Sakima anali kukhala ndi mlongo wake.

萨可满的父母在富人的家里工作。他们每天早出晚归,萨可满就和妹妹呆在家里。


Sakima anakonda kuimba nyimbo. Tsiku lina, amai ake anamufunsa, “kodi uphunzila kuti nyimbo izi, Sakima?”

萨可满很喜欢唱歌。有一天,他的妈妈问他:“萨可满,你从哪儿学了这些歌?”


Sakima anayankha, “zimabwela chabe, amai. Ndimazimvela m’mutu mwanga ndipo ndimaziimba.”

萨可满回答说:“它们就这样出现在我的脑海里,我想到了这些歌,就把它们唱了出来。”


Sakima anakonda kuimbila mlongo wake wam’gono, makamaka ngati anali wokwiya. Mlongo wake anamvelera ku nyimbo yake yapa mtima. Anatothozedwa.

萨可满很喜欢给他的妹妹唱歌,特别是她肚子饿的时候。妹妹听着萨可满唱他最喜欢的歌,跟着甜美的歌声摆动起来。


“Imbanso, Sakima,” mlongo wake anamupempha. Sakima ankavomela ndi kuimbanso mobwelezera.

萨可满的妹妹经常求他:“再唱一次吧!”萨可满唱了一遍又一遍。


Tsiku lina pamene makolo ake anbwelera ku nyumba, anakhala chete. Sakima anadziwa kuti kunali vuto.

有一天晚上,萨可满的父母回到家以后一句话也不说。萨可满知道一定发生了什么不好的事情。


“Kodi nichani chalakwika, amai, atate?” sakima anafunsa. Sakima anamvela kuti mwana wa bambo wolemera anasowa ndi bambo wake anali ndi chisoni.

萨可满问爸爸妈妈发生了什么事,他这才知道,原来富人的儿子失踪了,富人孤单一人,很伤心。


“Ndingawaimbile. Angakondwelenso,” Sakima anaudza makolo ake. Koma makolo ake sanamuvokeze naye. “Ndi munthu wolemela kwambiri. Iwe uli wa khungu chabe. Uganiza kuti nyimbo yako izamuthandiza?”

萨可满对父母说:“我可以给他唱歌,这样他就会高兴起来了。”但是萨可满的父母不喜欢这个主意:“他很有钱,而你只是一个看不见的小男孩。你以为你的歌声会帮到他吗?”


Angakhale choncho, Sakima sanaleke. Mlongo wake wamng’ono anamupasa mphamvu. Iye anati, “Nyimbo za Sakima zimandilimbikitsa pamene ndili okwiya. Zizalimbikitsanso bambo wolemela.

但是萨可满没有放弃,他的妹妹也鼓励他。她说:“萨可满的歌声能赶走饥饿,他肯定也能安慰富人。”


Tsiku lotsatilapo, Sakima anapempha mlongo wake kumupeleka ku nyumba ya bambo wolemela.

第二天,萨可满让他的妹妹带他去富人的房子。


Anaimilila pa pafupi ndi dzenera ndi kuyamba kimba nyimbo yake yapa mtima. Posachedwa, mutu wa bambo wolemela unayamba kuonekela pa dezenera lalikulu.

他站在一扇大窗户的下面,开始唱他最喜欢的歌。慢慢的,富人的脑袋从窗户里伸出来。


Anchito analeka zomwe anali kuchita. Anamvesela ku nyimbo ya Sakima yabwino. Koma bambo wina anati, “Kulibe omwe anakwanisapo kutonthoza akulu anchito. Kodi mnyamata wakhungu uyu aganiza kuti azawatonthoza?”.

工人们停下了工作。他们仔细地听着萨可满唱歌。有一个人说:“从来没有人能安慰老板,这个看不见的男孩觉得他可以做到吗?”


Sakima anasiliza kuimba nyimbo yake ndipo anatembenuka kufuna kubwelela kunyumba. Koma bambo wolemela atuluka naumuuza nati, “Chonde, imbanso nyimbo.”

萨可满唱完了,准备离开。富人跑出来,说:“请再唱一遍吧!”


Pa nthawi yomweyo, amuna awiri anabwela apo anyamula munthu. Anali anapeza mwana wa bambo wolemelayo atamenyedwa ndi kusiyidwa pambali pa mseu.

就在那时,两个人抬着担架走来了,担架上是富人的儿子!他们发现这个人被打得面目全非,躺在路边。


Bambo wolemela anakondwela kwambiri kuona mwana wake. Anapasa mphaso kwa Sakima powatonthoza. Anapeleka mwana wao ndi Sakima ku chipatala kuti Sakima akayambe kuonanso.

富人很高兴儿子找回来了。为了感谢萨可满安慰他,他把萨可满和他的儿子一起送到了医院,萨可满很快就会恢复视力了。


作者: Ursula Nafula
插图: Peris Wachuka
译文: Sitwe Benson Mkandawire
配音: Christine Mwanza
语言: 齐切瓦语
级别: 3级
出处: 原文来自非洲故事书Sakima's song
共享创意授权条款
本着作系采用共享创意 署名 4.0 未本地化版本授权条款授权。
选项
返回故事列表 下载 PDF