下载 PDF
返回故事列表

Mwana wa Bulu 驴孩子

作者 Lindiwe Matshikiza

插图 Meghan Judge

译文 David Sani Mwanza

配音 Christine Mwanza

语言 齐切瓦语

级别 3级

将整故事念出来 本故事尚未有语音版。


Kanali kamwana kakakazi kang’ono komwe kanaona chinthu cha maonekedwe odabwisa patali.

有个女孩最先发现了远处有个奇怪的身影。


Pamane chinthu chinabwela pafupi, anaona kuti anali mzimai ome anali ndi mimba yaikulu.

那个身影越靠越近,她看清楚了,那是一个快生孩子的妇女。


Mwamanyazi koma mopanda mantha, kamwana kayenda pafupi ndi mzimai. “Tifunika kukhala nao pamozi,” anthu a kamwana kakazi anavomekezana. “Tizamusunga ndi mwana wake bwino-bwino.

女孩有点儿害羞,但她还是勇敢地走上前去。和女孩随行的人们说:“我们必须和她呆在一起,我们必须保护她和她的孩子。”


Mwana anali pafupi kubadwa. “Kankha!” “Bwelesani zovimba!” “Water!” “Kankhaaaa!!!”

孩子很快就要降生了。“用力啊!”“快拿毯子来!”“水!”“再用点力!”


Koma pamene anaona mwana wakhanda, aliyense anabwelera m’mbuyo ndi kudabwa. “Bulu?!”

当他们看到孩子时,所有人都吓了一跳,“一头驴?”


Aliyense anayamba kukangana. “Tinakamba kuti tizamusunga pamozi ndi mwana wake bwino-bwino, ndipo tizachita motero,” ena anatero. “Koma azatibweretsera soka!” enanso ananena.

大家七嘴八舌吵起来。一些人说:“我们说过要保护母亲和孩子的,我们必须这样做。”但是还有一些人反驳说:“但是他们会给我们带来厄运。”


Chifukwa cha icho, mzimai anasala yekha. Anavutika kuganiza zomwe azachita ndi mwana wodabwisa. Anavutika kuganiza kuti azazichita chani.

妇女发现自己又孤零零一人了。她不知道该拿这个奇怪的孩子怎么办,她也不知道自己该怎么办。


Koma pothera, anafunika kuvomela kuti bulu anali mwana wake ndipo anali mai wake.

最后,她决定接受这个孩子,做他的妈妈。


Tsono, ngati mwana anakhala chimozimozi, ndi thupi ing’ono, zinthu zinakakhalako bwino. Koma bulu anakula ndi kukula kufikila nthawi yomwe sankakhala pa mbuyo pa mai wake. Ndipo mukhalidwe wake unasiyana ndi munthu. Amai ake anli olema nthawi zambili komanso aukali. Nthawi zina, anatuma mwana kuchita nchito zomwe zinafunikila kuchitika ndi nyama.

如果这个孩子一直这般大小,不长大的话,一切都会变得不一样。但是这个驴孩子越长越大,现在他再也不能趴在妈妈的背上。无论他多么努力,他始终不能像人类一样。他的妈妈累了,放弃了。有时候,她让他做一些动物会做的工作。


Msokonezo ndi mkwiyo unakula mu mtima wa bulu. Anali kulephela kuchita zilizonse. Analephela kukhali ndi mkhalidwe weni weni. Anali okwiya kotelo kuti, tsiku lina, anamenyesela amai ake pansi.

驴孩子感到迷茫,也很生气。他这个也不能做,那个也不能做。他不能这样,也不能那样。有一天,他太生气了,一脚把他的妈妈踹到地上。


Bulu anachita manyazi. Anayamba kuthawila kutali komwe angathe kupita.

驴孩子羞愧极了,他逃跑了,跑得越远越好。


Pa nthawi yamene analeka kuthawa, unali usiku, Bulu anasowa. “Hee, hyu?” anatelo ku mdima. Anafika pamathelo. Anayamba kusanduka. Anagona mu tulo twatukulu twa mavuto.

当他停下来的时候,天已经黑了,驴孩子迷路了。他在黑暗里哼哼,“咴咴”,黑暗中传来了回声,“咴咴”。他孤零零的一个人,卷成了一团,心中充满烦恼,沉沉地睡去。


Bulu anauka ndi kupeza nkhalamba ili kumuyangana. Anayangana mu maso a mdala ndi kuyamba kukhala ndi chiyembekezo.

驴孩子醒了,他发现有个老人低头盯着他。他看着老人的眼睛,感觉到了一丝希望。


Bulu afuna kukhala ndi mdala, omwe anamuphunzisa njira zambili zomwe angakhalilemo umoyo. Bulu anamva ndi kuphunzila, chimozi mozi mdala nayenso anamvesera ndi kuphunzila. Anathandizana ndipo anaseka pamozi.

驴孩子和老人住在一起,老人教会他很多生存的本领。驴孩子认真地听着,学得很快。老人也学了很多。他们互相帮助,遇到开心的事情就一起哈哈大笑。


Tssiku lina m’mawa, mdala anapempha Bulu kuti amunyamule kumupeleka pa mwamba pa phiri.

一天早上,老人让驴孩子带他到山顶。


Pamwamba pa mithambo, anagona. Bulu analota kuti amai ake anli kudwala ndipo anali kumuitana. Ndipo pamene anauka…

他们登上山顶,环绕在云雾中,睡着了。驴孩子梦到他的妈妈生病了,正在呼唤他,然后他就醒了……


Mithambo inachoka pamozi ndi mzake, mdala.

……云雾消失了,他的朋友——那个老人——也消失了。


Bulu anaziwa zomwe anafunika kuchita.

驴孩子终于知道要做什么了。


Buu anapeza amai ake, okha ali kulilila mwana wao wosowa. Anapenyana kwakanthawi, ndipo anakumbatilana mwamphamvu.

驴孩子找到了他的妈妈,她孤零零一个人,正在为走失的孩子伤心。他们互相打量了很久,然后紧紧地抱在了一起。


Bulu ndi amai ake akulila pamozi ndi anapeza nzila zosiyanasiyana zokhalilamo pamozi. Pang’ono pang’ono, onse anthu okhala pafupi nao ndi banja lao ayamba kukhala nao pamozi mopanda vuto lenileni.

驴孩子和妈妈住在一起,慢慢长大,学会了如何共同生活。渐渐的,其他的家庭也搬到他们附近,住了下来。


作者: Lindiwe Matshikiza
插图: Meghan Judge
译文: David Sani Mwanza
配音: Christine Mwanza
语言: 齐切瓦语
级别: 3级
出处: 原文来自非洲故事书Donkey Child
共享创意授权条款
本着作系采用共享创意 署名 4.0 未本地化版本授权条款授权。
选项
返回故事列表 下载 PDF