其他语言
中文
阿拉伯语
阿姆哈拉语
波兰语
波斯语
波斯语(阿富汗)
德语
俄语
法语
菲律宾语
韩语
孟加拉语
挪威语(书面)
挪威语(新)
旁遮普语
葡萄牙语
日语
斯瓦希里语
索马里语
土耳其语
乌尔都语
乌克兰语
西班牙语
意大利语
英语
粤语
越南语
藏语
更多语言…
返回故事列表
Nkhuku ndi Nkhwazi
母鸡和老鹰
Ann Nduku
Wiehan de Jager
Sitwe Benson Mkandawire
Christine Mwanza
本故事尚未有语音版。
Panali-panali, nkhuku ndi nkhwazi anali abwenzi. Anakhala mumutendele ndi mbalame zina. Panalibe paiwo amene anali kuuluka.
很久很久以前,母鸡和老鹰是好朋友。他们和其他的鸟儿住在一起,相安无事,但是他们都不会飞。
Tsiku lina, kunali njala kudziko. Nkhwazi anali kuyenda kutali kukasakila cakudya. Anabwelako olema kwambili. “Kufunikila kukhala njila ina yapafupi mumayendedwe” Nkhwazi inatelo.
有一天,他们住的地方发生了饥荒。老鹰要走很远很远的路才能找到食物。她回来的时候看起来非常疲倦。老鹰说:“这样走太累了!肯定有一种更省力的方法。”
Mumawa mwace, nkhuku inali ndi ganizo labwino. Inayamba kutola nthenga za mbalane iliyonse yamene inagwa. “Tiyeni tisokele pamodzi na nthenga zamene tili nazo” inatelo nkhuku. “Mwina ici cidzakhala capafupi kuyenda.”
母鸡饱饱地睡了一觉,想到了一个好主意。她开始搜集其他鸟儿掉下来的羽毛,说:“让我们把这些羽毛都缝在我们身上吧,也许这样我们走路就不吃力了。”
Nkhwazi ndiye anali cabe ndi nsingano yotungila pamudzi, iye anayambilila kusoka. Anazipangila mapiko awili abwino-bwino nakuuluka pamwamba pa nkhuku. Nkhuku inabweleka nsingano koma analema kutunga. Anasiya nsingano yosokela pa kabati ndipo anayenda kukakonza cakudya ca ana ake ku khicini.
老鹰是村庄里唯一一个有银针的,所以她第一个开始缝羽毛。她给自己做了一双非常漂亮的翅膀,做完之后,在母鸡头上飞来飞去。母鸡问老鹰借了针,但她很快就厌烦了缝纫。她把银针留在柜子上,跑到厨房里,给她的孩子做饭。
Mbalame zina zinaiona nkhwazi kuuluka. Zinafunsa nkhuku kuti iwabweleke nsingano kuti zipangile mapiko youlukila nao. Mosacedwa, kunali mbalame zambili kuuluka mumwamba.
其他的鸟儿看到老鹰飞得又高又远,非常羡慕。他们问母鸡借了银针,这样他们也可以给自己做翅膀了。过了不久,其他的鸟儿也都能上天飞翔了。
Pamene mbalame yomalizila inabweza nsingano yosokela, nkhuku panalibe. Ana a nkhuku anatenga nsingano nakuyamba kusowela nayo. Pamene analema kusowela, anasiya nsingano ija mumcenga.
当最后一只鸟儿归还银针的时候,母鸡不在家。她的孩子拿走了银针,玩来玩去。他们玩厌的时候,就把银针落在了沙地里。
Mumazulo, nkhwazi anabwelela. Anapempha nsingano kuti asokele nthenga zimene zinasokomoka paulendo. Nkhuku inasakila nsingano pakabati, mophikila, ndi panja pa nyumba. Koma nsingano sinapezeke.
那天下午,老鹰回来了,她问母鸡要回自己的银针,因为她要修补一些松散的羽毛。母鸡找遍了柜子、厨房和后院,都找不到银针。
“Ndipatseni tsiku limodzi” Nkhuku inapempha nkhwazi. “Kuti mukakonze phiko lanu ndikuulukanso kukasakila cakudya.” “Tsiku limodzi cabe” Nkhwazi anatelo. “Ngati siupeza nsingano, uzandipatsa mwana wako m’modzi kukhala malipilo.”
母鸡求老鹰:“再给我一天吧!明天你就能修补翅膀,飞着去找食物了。”老鹰说:“好,就一天。如果你找不到银针的话,你就要把一个孩子给我作为补偿。”
Pamene nkhwazi inabwela tsiku lotsatilapo, anapeza nkhuku asakilabe mumcenga, koma nsingano sanaipeze. Nkhwazi anauluka mwamsanga ndikugwila kamwana ka nkhuku kamodzi. Anapita nako kutali. Kucokela nthwiyo, nkhwazi ikaonekela cabe, iona nkhuku isakila nyeleti mumicenga.
第二天,老鹰来了,她看到母鸡正在沙地里翻来翻去,但是银针还是没有找到。老鹰从天上俯冲下来,抓了一只小鸡就飞走了。从那以后,无论老鹰什么时候出现,她都看到母鸡在沙地里找银针。
Ngati mthunzi wa phiko ya nkhwazi waonekela kucoka kumwamba, Nkhuku icenjeza ana ake. “Cokani poonekela.” Ndiponso iwo akuyankha, “Sindife oputsa, tizathamanga.”
当母鸡在地上看到老鹰的影子时,她就警告自己的孩子:“快躲起来!别呆在这空旷干燥的地上。”孩子们回答她说:“我们不是傻瓜,我们会跑的。”
作者: Ann Nduku
插图: Wiehan de Jager
译文: Sitwe Benson Mkandawire
配音: Christine Mwanza