其他语言
中文
阿拉伯语
阿姆哈拉语
波兰语
波斯语
波斯语(阿富汗)
德语
俄语
法语
菲律宾语
韩语
孟加拉语
挪威语(书面)
挪威语(新)
旁遮普语
葡萄牙语
日语
斯瓦希里语
索马里语
土耳其语
乌尔都语
乌克兰语
西班牙语
意大利语
英语
粤语
越南语
藏语
更多语言…
返回故事列表
Kambewu: Nkhani ya Wangari Maathai
一粒小种子:旺加里·马塔伊的故事
Nicola Rijsdijk
Maya Marshak
Gridon Mwale
Christine Mwanza
本故事尚未有语音版。
Pamudzi wina womangidwa pamatero ya phiri la Kenya kumwawa kwa Africa, Kunali kamtsikana kena dzina lake Wangari. Wangari ndi amai ake anali kugwira ntchito zaminda.
在东非肯尼亚山的山腰上,有一座小村庄,村庄里有一个小女孩和妈妈一起在田里劳作,这个女孩叫旺加里。
Wangari anali mtsikana wokonda kucezera pabwalo. Tisku lina Wangari anagaula mudimba mwao nabzyala tumbewu pansi pomwe panali potentha kwambiri.
旺加里很喜欢呆在户外。在她家的农田里,旺加里用弯刀劈开土地,把小种子播撒到温暖的泥土里。
Thawi imene anali kukonda kwambiri mtsikanayu tsiku lililonse inali pamene dzuwa litangolowa kumene. Ndipo mudima ukagwira chakuti zomera zamthengo zaleka kuoneka, Wangari anali kudziwa kuti thawi yopita ku nyumba yafika tsopano. Ndipo popita kunyumba anali kudzera njira zang’ombe, kuwoloka mitsinje ndi kudutsa minda mpaka kufika kwao.
她一天中最喜欢的时候就是日落时分。当天黑了,看不到花花草草时,旺加里就知道她该回家了。她走在农田里的小路上,还要过几条河。
Wangari anali mwana wocenjera kwambiri ndipo anali wofunitsitsa kupita kusukulu kukaphunzira. Koma makolo ake sanafune kuti kamtsikana aka kaphunzire koma kazikhala pa nyumba ndi kugwira ncthito. Pamene Wangari anali ndi zaka 7, mukulu wake wamwamuna anagonjetsa makolo awo pokambirana kuti Wangari apite kusukulu akaphunzire.
旺加里是个聪明的孩子,她迫不及待地想要去上学,但是她的父母希望她能在家,帮着干农活。当旺加里七岁的时候,她的哥哥说服了父母,让旺加里去上学。
Wangaari anakonda kuphunzira kwambir chotero kuti anaphunzira kopitirira kupyolera mkuwerenga mabuku osiyanasiyana. Ndipo anakhoza kwambiri pa sukulu chotero kuti anapeza umwayi wokaphunzira ku dziko lakutali la United States of America. Wangari anasangalala kwambiri chifukwa anali kufunitsitsa kudziwa zambiri zapa dziko lapansi.
旺加里太喜欢学习了。旺加里读了很多书,学到很多知识。她的成绩非常好,最后收到了美国大学的录取信,邀请她去美国读书。旺加里太兴奋了,她真想去世界各地走走看看。
Wangari anaphunzira zinthu zambiri pamene anali pa American Univeziti. Anaphunzira pa zomera ndi mumene zimakulira. Zimenezi zinamukumbutsa mumene anali kusewerera ndi abale ake mthunzi ya mitengo mthengo laku-dziko lokongola la Kenya.
在美国的大学里,旺加里学到了很多新鲜事物。她研究植物,以及它们的生长过程。她想起她自己是怎么长大的:她和兄弟们在美丽的肯尼亚森林里玩耍。
Pamene anali kuphunzira tsiku ndi tsiku anazindikira kuti akonda anthu akwao ku Kenya. Anali kufuna kuti anthu kudziko limeneli tsiku lina akapate ufulu ndi mtendere. Ndipo anayewa dziko lakwao pamene anapitiliza ndi maphunziro. ake kwakanthawi.
她学得越多,就越热爱肯尼亚人民。她想要帮助肯尼亚人民过上自由、快乐的生活。她学得越多,就越想念自己在非洲的家乡。
Anabwerera kudziko lakwao ku Kenya pamane anamaliza maphunziro ake ndipo nthawi imeneyi dziko la Kenya linali litasintha. Mapulazi akuluakulu anatenga malo ochuluka. Azimai anali kusowa kotheba nkhuni chifukwa mitengo kunalibe. Anthu anali osauka ndipo ana anali kuoneka anjala.
当旺加里完成学业时,她回到了肯尼亚,但是她的祖国已经今非昔比了。大地上建起了农场,妇女们找不到柴火做饭。人们过着穷苦的日子,孩子们饥肠辘辘。
Wangari anali kudziwa chofunika kuchita kuti athetsa mabvuto amenewa: anaphunzitsa azimai kubzyala mitengo kuchokera kumbewu. Azimai amenewa anayamba kugulitsa mitengo zao zitakula ndikupeza ndalama zosamalira ma banja awo. Chifukwa cacimenechi azimai anakhala wokondwera kwambiri ndi Wangari amene anawa thandiza kuti akhale ndi mphanvu komanso olimba.
旺加里知道自己要做什么。她教妇女们如何用种子种出大树。妇女们卖树赚钱,补贴家用。妇女们都很高兴。旺加里使她们觉得自己变得坚强勇敢了。
Patapita zaka zambiri, mitengo zimene zinabzyalidwa zija, zinakula ndi ku panga thengo. Mitsinje inayambanso kukhala ndi madzi. Mbiri ya Wangari inafika ponseponse mu Africa. Lerolino, mitengo zamitundumitundu mamilyoni tilikuonazi zinachokera ku mbewu ya Wangari.
时光飞逝,小树长成了参天大树,又汇聚成了森林,河水穿流而过。旺加里的办法传遍了非洲。今天,因为旺加里当初的种子,已经长出了几百万棵大树。
Wangari anasewenzadi mwamphanvu. Chotero kuti anthu dziko lonse lapnansi anazindikila ntchito yaikula yomwe anacita, ndipo ana patsidwa mphoto yodziwika kwambiri padziko lonse lapansi. Mphoto imeneyi inali kutchedwa kuti Kulemekezedwa ndi Mtendere, ndipo anakhala mkazi woyamba mu Africa kulandila mphoto yotero.
旺加里努力工作,引起了全世界的注意,人们授予她诺贝尔和平奖,她是非洲第一位获得这份殊荣的女性。
Wangari anamwalira mu caka ca 2011, koma timamukumbukila tikamaona mtengo wokongola uliwonse mthengo.
旺加里在2011年去世,但是每次我们看到大树时,都会想起这位杰出的女性。
作者: Nicola Rijsdijk
插图: Maya Marshak
译文: Gridon Mwale
配音: Christine Mwanza