Back to stories list

Magozwe Magozwe Magozwe

Written by Lesley Koyi

Illustrated by Wiehan de Jager

Translated by Bether Mwale Moyo

Read by Christine Mwanza

Language Nyanja

Level Level 5

Narrate full story The audio for this story is currently not available.


Mu tauni ya Nairobi, kutali ndi umoyo wosungidwa bwino kunyumba, kunali kukhala anyamata analibe mabanja. Anangokhala mwa tsiku momwe ingabwerere. Tsiku lina m’mawa, anyamata anali kulonga mpasa zao pambuyo pogona pampepo mumbali mwa museu. Kusewenzesa vinyalala, anayasa moto kuti adziteyteze ku mphepo. Pagulu la anyamata iri panali Magozwe. Iye ndiye anali wamung’ono.

In the busy city of Nairobi, far away from a caring life at home, lived a group of homeless boys. They welcomed each day just as it came. On one morning, the boys were packing their mats after sleeping on cold pavements. To chase away the cold they lit a fire with rubbish. Among the group of boys was Magozwe. He was the youngest.

Mwi tauni lya Nairobi, ukutali ne ndupwa ishabasakamene, mwaleikala abalumendo abashakwete amayanda. Baaleikalafye cikulu bwaca. Uluceelo lumo, abalumendo baaleelonga impasa shabo panuma yakulaala mumpepo mumbali yanshila. Ukubomfya ifisooso, baalikoseshe umulilo pakupwisha impepo. Pali ili bumba paali Magozwe. Ewaali umwaice saana.


Pomwe makolo ake Magozwe anamwalira, iye anali ndia zaka cabe zisanu. Ndipo anapita kukakhala ndi amalume ake. Amalume ake sanamusamalirebwino mwanayu. Sanali kumupatsa cakudwa cokwanira Magozwe. Ndipo anali kugwiritsa nchito zambiri zolimba.

When Magozwe’s parents died, he was only five years old. He went to live with his uncle. This man did not care about the child. He did not give Magozwe enough food. He made the boy do a lot of hard work.

Ilyo abafyashi bakwa Magozwe baafwile, aalifye ne myaka isaano. Aile mukwikala na banalume. Banalume tabapooseleko amaano kuli Magozwe. Taabaaleemupeela ifyakulya ifyakumanina. Baaleemupeela incito shakubomba ishingi.


Ngati Magozwe wafunsa mwina wadandaula, amalume ake anali kumumenya. Pomwe anafunsa kuti apite kusukulu, amalume ake anamumenya nanena nati “Ndiwe citsiru kwambiri sungaphunzire kalikonse.” Patapita zaka zitatu zosungidwa mwankhanza, Magozwe anathawa kucoka pa nyumba pa amalume ake. Anayamba kukhala m’mseu.

If Magozwe complained or questioned, his uncle beat him. When Magozwe asked if he could go to school, his uncle beat him and said, “You’re too stupid to learn anything.” After three years of this treatment Magozwe ran away from his uncle. He started living on the street.

Nga Magozwe ati epushe nangu ukuilishanya, banalume baaleemuma. Ilyo Magozwe aipwishe palwa kuya ku sukulu, banalume baalimumine kabili baatiile, “Iwe tawakwata amaano. Tapali ico wingasambilila.” Panuma ya myaka itatatu iyakumusunga muli uyu musango, Magozwe aalibuutwike ukufuma pa ŋanda yaba nalume. Aatampile ukwikala mu musebo.


Kunali kobvuta kukhala kwa m’mseu ndipo anyamata ambiri anali kubvutika masiku onse kupeza cakudya. Masiku ena anamenyedwa, nthawi zina anagwiridwa ndi apolisi. Akadwala kunalibe munthu owathandiza. Ndalama zomwe anapeza mukupempa pempha, kugulitsa ma pulasitiki ndi zina, ndiye ndalama zomwe zinali kuwathandizira. Umoyo unabvutirako cifukwa magulu ena a anyamata anali kufuna kulanda malo osiyana-siyana mu tauni.

Street life was difficult and most of the boys struggled daily just to get food. Sometimes they were arrested, sometimes they were beaten. When they were sick, there was no one to help. The group depended on the little money they got from begging, and from selling plastics and other recycling. Life was even more difficult because of fights with rival groups who wanted control of parts of the city.

Ukwikala mu musebo kwali ukwayafya kabili abalumendo abengi baaleecuula cila bushiku pa kusanga icakulya. Inshiku shimo baaleebooma, shimbi baaleebeekata kuli bakapokola. Nga baalwala takwaleeba abakubaafwa. Ulupiya baaleesanga mu kulombalomba, mu kushitisha amapulasitiki na fimbi elwaleebaafwilishako. Ubuumi bwalyafisheko pantu amabumba yambi ayabalumendo yaaleefwaya ukupoka incende shapusanapusana mu tauni.


Tsiku lina pamene Magozwe anali kusakira-sakira muvinyalala, anapeza buku lina losira long’ambika. Anacosako madoti ndipo analiika mu nsaka. Tsiku lirironse lotsatira, anatulutsa bukulo ndipo anayamba kuona zitunzi-thunzi mu bukulo. Sanali kudziwa kuwerenga mau.

One day while Magozwe was looking through the dustbins, he found an old tattered storybook. He cleaned the dirt from it and put it in his sack. Every day after that he would take out the book and look at the pictures. He did not know how to read the words.

Ubushiku bumo ilyo Magozwe aaleefwayafwaya mu fisooso, aasangile ibuuku ilyakale ilyalepauka. Aafumisheko ifiko aalibika na mwisaaka. Cila bushiku, aleefumya ibuuku no kwamba ukulolesha pa fikope. Taishibe ukubelenga.


Zithunzi-thunzi zinalangiza mnyamata emwe anakula kukhala oyendetsa ndeke. Magozwe analota ndi msana momwe, kukhala oyendesa ndeke. Nthawi zina anaziona kuti ndiye amene anali mnyamata wamubuku muja.

The pictures told the story of a boy who grew up to be a pilot. Magozwe would daydream of being a pilot. Sometimes, he imagined that he was the boy in the story.

Ifikope fyaleelanga umulumendo uwaishileba kensha wandeke ilyo aakulile. Magozwe aaleeloota palwa kuba kensha wandeke na mu kasuba. Inshita shimo aleemona ukuti emulumendo wine uwa mwibuku.


Kunali kozizira ndipo Magozwe anaimirira m’mseu kupempha-pempha. Bambo wina anabwera pafupi naye. “Bwanji, ndine Thomas. Ndisewenza pafupa ndi pano, pamalo pamene ungapeze cakudya,” anatero bamboyo. Analoza nyumba yacikasu, ya tsindwi yamtambo. “Ndikhulupiriraa udzapitako kuti utengeko cakudya?” anafunsa. Magozwe anayangana bambo nayangana nyumba. “Kapena ndidzapita,” anayanka, ndipo anacokapo.

It was cold and Magozwe was standing on the road begging. A man walked up to him. “Hello, I’m Thomas. I work near here, at a place where you can get something to eat,” said the man. He pointed to a yellow house with a blue roof. “I hope you will go there to get some food?” he asked. Magozwe looked at the man, and then at the house. “Maybe,” he said, and walked away.

Kwalitaleele kabili Magozwe aiminine pa musebo aleelombalomba. Umwaume umo aishile mupeepi napo aali. “Uli shaani? Nine Thomas. Momba mupeepi napano, pa ncende wingapoka icakulya,” efyo aasosele. Asontele ku ŋanda iyamutuntula no mutenge wa makumbi-makumbi. “Ndesubila walaayapoka ifyakulya?” efyo aipwishe. Magozwe aaloleeshe Thomas elyo kabili aloleesha ku ŋanda. “Limbi ndeeya,” efyo ayaswike, afumanapo.


Patapita Miyezi ingapo yotsatira, anyamata osowapokhala anazolowera kuonana ndi Thomas. Thomas anali kukonda kukamba ndi anthu maka-maka anthu okhala m’miseu. Thomas amamvetsera nkhani za anthu awa. Anali wacidwi ndipo wokhadzikika mtima, ndiponso sanataye ulemu. Anyamata ena anayamba kupita kunyumba yacikasu ya tsindwi yamtambo kukatenga cakudya masana.

Over the months that followed, the homeless boys got used to seeing Thomas around. He liked to talk to people, especially people living on the streets. Thomas listened to the stories of people’s lives. He was serious and patient, never rude or disrespectful. Some of the boys started going to the yellow and blue house to get food at midday.

Imyeshi yakonkelepo, abalumendo baalibeeleshe ukumona Thomas. Alitemenwe ukulanda na bantu maka-maka abaaleikala mu musebo. Thomas aaleumfwa ilyashi pa buumi bwa aba bantu. Aaleepoosa amaano ku fintu kabili uwacikuuku no mucinshi. Abalumendo bamo, bayambile ukuya ku ŋanda ya mutuntula na Makumbi-makumbi mukupoka ifyakulya akasuba.


Magozwe anali nkhale mumbali mwa mseu akuyangana zithunzi-tunzi mu buku yake pamene Thomas anabwera nakhala pafupi naye. “Kodi nkhani Ikamba za ciani?” anafunsa Thomas. “Ikamba pa za mnyamata amena anakhala oyendesa ndeke,” anayankha Magozwe. “Nindani dzina lake mnyamatayo?” anafunsa Thomas. “Kaya, sindidziwa kuwerenga,” anayankha Magozwe mwakacetecete.

Magozwe was sitting on the pavement looking at his picture book when Thomas sat down next to him. “What is the story about?” asked Thomas. “It’s about a boy who becomes a pilot,” replied Magozwe. “What’s the boy’s name?” asked Thomas. “I don’t know, I can’t read,” said Magozwe quietly.

Magozwe aikele mumbali yanshila aleetamba ifikope mwibuuku lyakwe ilyo Thomas aishileikala mupeepi nankwe. “Lileelanda pali cinshi ilyashi?” efyo Thomas aipwishe. “Lileelanda pa mulumendo uwaishileba kensha wandeke,” efyaaswike Magozwe. “Naani ishina umulumendo?” efyaipwishe Thomas. “Katwishi, nshaishiba ukubelenga,” efyayaswike Magozwe mwishiwi lya panshi.


Pomwe anakumana, Magozwe anayamba kuuza Thomas, nkhani za umoyo wake. Anamuuza za mwamene anathawira kucoka kwa amalume ake. Thomas sanakambe zambiri, ndipo sanauze Magozwe zocita koma anamvetsera mwacidwi. Nthawi zina Magozwe ndi Thomas anakambirana pamene anali kudya munyumba ya tsindwi yamtambo.

When they met, Magozwe began to tell his own story to Thomas. It was the story of his uncle and why he ran away. Thomas didn’t talk a lot, and he didn’t tell Magozwe what to do, but he always listened carefully. Sometimes they would talk while they ate at the house with the blue roof.

Ilyo baakumeene, Magozwe aatendeke ukweba Thomas ilyashi pa buumi bwakwe. Aamwebele ifyo aabuutwike ukufuma kuli banalume. Thomas taalaandile ifingi kabili taebele Magozwe ifyakucita lelo aaleumfwikishafye. Limo-limo baaleelanshanya ilyo baleelya mu ŋanda yamutenge wa Makumbi-makumi.


Pomwe Magozwe anali pafupi ndikukwanitsa zaka khumi, Thomas anamupatsa buku. Buku inali pa za mnyamata wa m’mudzi amene anakula kukhala womenya bola odziwika kwambiri. Thomas anamuwerengera Magozwe kambiri, mpaka tsiku lina anakamba nati, “Niganiza kuti uyambe kupita ku sukulu, kuti ukaphunzire kuwerenga. Uganizapo bwanji?” Thomas ananena kuti anali kudziwa malo kumene ana angapite kukhala ndiponso kuphunzira kwameneko.

Around Magozwe’s tenth birthday, Thomas gave him a new storybook. It was a story about a village boy who grew up to be a famous soccer player. Thomas read that story to Magozwe many times, until one day he said, “I think it’s time you went to school and learned to read. What do you think?” Thomas explained that he knew of a place where children could stay, and go to school.

Ilyo Magozwe aali ne myaka ikumi, Thomas alimupeele ibuuku. Ibuuku lyali pa mulumendo wa mumushi uwaleeteya umupila uwalumbwike saana. Thomas alibelengeele Magozwe ili lyashi imiku iingi mpakafye bushiku bumo atiile, “Ndetontonkanya ukuti ulingile ukutampa isukulu pakuti usambilile ukubelenga. Uleetipo shani?” Thomas atiile alishibe incende uko abaana bengalaikala no kuya ku sukulu.


Magozwe anaganizira za kumalo atsopano komweko ndiponse zakupitaa ku sukulu. Nanga kapena amalume ake anakamba zoona kuti anali citsiru kwambiri ndipo sangapunzire kalikonse? Nanga ngati bamumenya kumalo atsopanowa? Anayopa. “Kapena ciribwino kupitiriza kukhala pa m’seu,” anaganiza.

Magozwe thought about this new place, and about going to school. What if his uncle was right and he was too stupid to learn anything? What if they beat him at this new place? He was afraid. “Maybe it is better to stay living on the street,” he thought.

Magozwe aatontonkenye pali ii ncende iipya na palwa kuya ku sukulu. Nga limbi ifyo banalume bamwebele ukuti taakwata amaano teeti asambilile icili conse fyaciine? Nga cakuti kulya kuncende bamuuma? Alitiinine. “Limbi cawamapo ukutwalilila ukwikala mu musebo,” efyo aatontonkenye.


Anamuuza Thomas kuti anali ndi mantha. Thomas anamusimikidzira kuti, azakhala ndi umoyo wabwina kumalo atsopanowa.

He shared his fears with Thomas. Over time the man reassured the boy that life could be better at the new place.

Aebele Thomas ati aali no mwenso. Thomas nao alimukoseleshe ukuti akeekalafye bwino kuncende ilya.


Motero Magozwe anapita kukhala mu cipinda mu nyumba ya tsindwi yamsipu. Anakhala ndi anyamata ena awiri mu cipinda. Pamodzi onse anali anyamata khumi amene anali kukhala panyumba paja. Pamodzi ndi a Anti Cissy ndi amuna ao, agalu atatu, cona ndi mbuzi yokalamba.

And so Magozwe moved into a room in a house with a green roof. He shared the room with two other boys. Altogether there were ten children living at that house. Along with Auntie Cissy and her husband, three dogs, a cat, and an old goat.

Efyo Magozwe aile mukwikala mu muputule mu ŋanda yamutenge wa katapa-katapa. Aaleikalamo na balumendo bambi babili. Abaana bonse pamo abaleeikala muli ilya ŋanda baali ikumi. Elyo naba maama Cissy na balume baabo ne mbwa shitatu, puushi elyo ne mbushi iikote.


Magozwe anayamba sukulu ndipo cinali cobvuta. Ndizambiri zimene anali kufunikira kudziwa kuti alingane ndi anzake. Nthawi zina anali kufuna kuleka. Koma anaganizira oyendetsa ndeke ndi omenya bola a mu mabuku ake anthano. Monga iwo anyamata a mu mabuku, sanaleke.

Magozwe started school and it was difficult. He had a lot to catch up. Sometimes he wanted to give up. But he thought about the pilot and the soccer player in the storybooks. Like them, he did not give up.

Magozwe alyambile isukulu kabili lyalikosele. Fiingi ashaishibe ifyo aalingile ukwishiba pakuti alingane na banankwe. Limo-limo aaleefwaya no kuleka isukulu. Leelo aaleetontonkanyo pali kensha wandeke na kateya wa mupila abamumabuuku yakwe. Taalekele nga filya fine nabo bashalekele.


Magozwe anali khale panja panyumba ya tsindwi ya msipu, akuwerenga buku lake lakusukulu, Thomas anabwera ndi kukhala pafupi naye. “Ikamba ciani nkhani uwerenga?” anafunsa Thomas. “Ikamba pa za mnyamata amene anakhala mphunzitsi,” anayankha Magozwe. “Ndani dzina munyamata?” anafunsa Thomas. “Dzina lake ndi Magozwe,” anayankha Magozwe momwetula.

Magozwe was sitting in the yard at the house with the green roof, reading a storybook from school. Thomas came up and sat next to him. “What is the story about?” asked Thomas. “It’s about a boy who becomes a teacher,” replied Magozwe. “What’s the boy’s name?” asked Thomas. “His name is Magozwe,” said Magozwe with a smile.

Magozwe aikeele panse pa lubansa lwa ŋanda ya mutenge wa katapa-katapa, aleebelenga ibuuku lyaku sukulu. Thomas nao aishile ikala mupeepi nankwe. “Lilelanda pali cinshi ilyashi?” efyaipwishe Thomas. “Lileelanda pa mulumendo awaishileba kafundisha,” efyayaswike Magozwe. “Naani ishina umulumendo?” efyaipwishe Thomas. “Ishina lyakwe ni Magozwe,” efyalandile Magozwe ninshi aleemwentula.


Written by: Lesley Koyi
Illustrated by: Wiehan de Jager
Translated by: Bether Mwale Moyo
Read by: Christine Mwanza
Language: Nyanja
Level: Level 5
Source: Magozwe from African Storybook
Creative Commons License
This work is licensed under a Creative Commons Attribution 4.0 International License.
Read more level 5 stories:
Options
Back to stories list Download PDF