Schaltfläche PDF
Zurück zur Geschichteliste

Cuti Kwa Ambuya Ferien mit Großmutter

Geschrieben von Violet Otieno

Illustriert von Catherine Groenewald

Übersetzt von Bether Mwale Moyo

Gelesen von Christine Mwanza

Sprache Nyanja

Niveau Niveau 4

Vollständige Geschichte erzählen Zu dieser Geschichte ist noch kein Audio verfügbar.


Odongo ndi Apiyo anali kukhala mu tauni ndi atate awo. Amakondwerera masiku acuti. Sikuti Kamba kakuti masukulu anatsekera, koma cifukwa amapita kwa agogo. Awo Agogo awo anali kukhala m’mudzi wogwira nsomba pafupi ndi nyanja yaiukulu.

Odongo und Apiyo lebten mit ihrem Vater in der Stadt. Sie freuten sich auf die Ferien. Nicht nur weil sie dann nicht in die Schule mussten, sondern auch weil sie dann ihre Großmutter besuchen würden. Sie lebte in einem Fischerdorf in der Nähe eines großen Sees.


Odongo ndi Apiyo anali okondwera cifukwa inali nthawi yokayenderanso agogo awo. Usiku wa ulendo usanacitike, analongelato katundu kukonzekela ulendo wautali kupita kumudzi. Usiku uyu, anawa, sanagone ndipo anacezera kulankhula usiku wonse pa za cuti.

Odongo und Apiyo freuten sich, dass es Zeit war ihre Großmutter zu besuchen. Am Abend davor packten sie ihre Taschen und bereiteten sich für die lange Reise zu ihrem Dorf vor. Sie konnten nicht schlafen und redeten die ganze Nacht über den Urlaub.


Kuseni seni anayambapoM’mamawa kutaca, ulendo unapangika wopita kumudzi mgalimoto ya atate awo. Anayenda kupitirira mapiri, nyama zamuthengo ndi minda ikulu-ikulu kwambiri. Ana awa, anawelenga magalimoto munjira ndipo anayimba nyimbo.

Früh am nächsten Morgen machten sie sich im Auto ihres Vaters zum Dorf auf. Sie fuhren an Bergen, wilden Tieren und Teeplantagen vorbei. Sie zählten Autos und sangen Lieder.


Patapita nthawi, ana awa analema ndipo anagona.

Nach einer Weile waren die Kinder müde und schliefen ein.


Pamene anafika mu mudzi, atate awo anautsa Odongo ndi Apiyo. Anapeza Nyar-Kanyada, ambuya awo aligone pa mpasa munsi mwa mutengo. Nyar-Kanyada muciruo, atanthauza kuti “mwana wamkazi wa a Kanyada”. Ambuya awo anali muzimai wampamvu, ndipo wokongola kwambiri.

Vater weckte Odongo und Apiyo, als sie im Dorf ankamen. Nyar-Kanyada, ihre Großmutter, lag auf einer Matte unter einem Baum und entspannte sich. Nyar-Kanyada in Luo bedeutet „Tochter des Volkes von Kanyada“. Sie war eine schöne und starke Frau.


Ambuya anakondwera kwambiri ndipo anavina vina, nayimba nyimbo zacisangalalo. Azukulu nawo anakondwera kwambiri, ndipo anapasa ambuya awo mpaso zomwe anawabwelesela. “Yambirirani kusegula yanga mpaso,” anati Odongo. “Yambirirani yanga,” anati Apiyo.

Nyar-Kanyada bat sie ins Haus und tanzte freudig im Zimmer herum. Ihre Enkelkinder überreichten ihr begeistert ihre Geschenke. „Öffne mein Geschenk zuerst“, meinte Odongo. „Nein, meins zuerst!“, entgegnete Apiyo.


Pomwe anasegula mpaso, Ambuya awo anawadalisa azukulu awo monga mwa mwambo.

Nachdem sie die Geschenke geöffnet hatte, segnete Nyar-Kanyada ihre Enkelkinder auf traditionelle Art.


Ndipo Odongo na Apiyo anayenda panja nayamba kupirikisa ma bulaula na mbalame.

Dann gingen Odongo und Apiyo nach draußen. Sie jagten Schmetterlingen und Vögeln nach.


Ana awa, anakwera mitengo ndipo anasewera m’madzi amnyanja.

Sie kletterten auf Bäume und planschten im See.


Pamene kunada, ana anabwerera kunyumba kukadya cakudya ca madzulo. Koma akalibe kutsiriza kudya, anayamba kumva tulo!

Als es dunkel war, gingen sie zum Abendessen ins Haus zurück. Noch bevor sie fertig waren, schliefen sie ein.


M’mawa mwake, atate awo a Odongo ndi Apiyo anabwerera ku tauni ndikuwasiya ndi ambuya awo Nyar-Kanyada.

Am nächsten Tag fuhr der Vater zurück in die Stadt und ließ die Kinder bei Nyar-Kanyada.


Odongo ndi Apiyo anathandiza ambuya awo nchito za panyumba. Ana awa anatunga madzi ndi kusakira nkhuni. Anatola mazira ankhuku ndi kuthyola ndiyo m’dimba.

Odongo und Apiyo halfen ihrer Großmutter im Haushalt. Sie holten Wasser und Feuerholz. Sie sammelten Eier von den Hühnern und ernteten Gemüse aus dem Garten.


Ambuya awo anapunzisa adzukulu awo kuphika nsima, nsomba, ndi ndiyo zina zakumudzi.

Nyar-Kanyada lehrte ihre Enkelkinder, wie man weichen Ugali als Beilage für den Eintopf zubereitet. Sie zeigte ihnen, wie man Kokosreis als Beilage zum Bratfisch macht.


Tsiku lina,, Odongo anapita kukadyetsera ng’ombe. Ng’ombe zina zinalowa m’munda mwa anthu ena. Mlimiyu anakalipira Odongo kwambiri. Anaopseza kuti adzasunga pakudya mbewu zake. Patapita tsikulo, munyamata anatsimikidza kuti ng’ombe zisakhalenso mumabvuto.

Eines Morgens brachte Odongo Großmutters Kühe zum Grasen. Sie liefen hinüber zur Nachbarsfarm. Der Bauer war sehr böse auf Odongo. Er drohte, die Kühe als Entschädigung zu behalten. Von dort an passte der Junge genau auf, dass die Kühe keine Schwierigkeiten mehr machten.


Tsiku linanso, ana anapitaa ku musika ndi ambuya awo. Anali ndi stolo yogulitsamo ndiyo za m’munda, shuga ndi sopo. Apiyo anali kukonda kuuza anthu ogulamitengo ya zinthu. Odongo anali kukonda kulongeza zinthu zimene anthu anali kugula.

An einem anderen Tag gingen die Kinder mit Nyar-Kanyada zum Markt. Sie hatte einen Stand, wo sie Gemüse, Zucker und Seife verkaufte. Apiyo hatte Spaß dabei, den Kunden die Preise für Dinge zu nennen. Odongo packte die Artikel ein, die die Kunden kauften.


Pakuthera kwa tsiku anali kumwa tiyi ya chai pamodzi. Anathandiza ambuya awo kuwerenga ndalama zimene analinazo.

Am Ende des Tages tranken sie einen Chai-Tee zusammen. Sie halfen Großmutter, das eingenommene Geld zu zählen.


Koma mosacedwa cuti cinali kutha ndipo ana amafunika kubwerera ku tauni ir. Ambuya anapatsa Odongo kapu ndipo anapatsa Apiyo juzi. Ambuya analonga cakudya capaulendo.

Aber all zu schnell waren die Ferien zu Ende und die Kinder mussten in die Stadt zurückkehren. Nyar-Kanyada gab Odongo eine Kappe und Apiyo ein Sweatshirt. Sie packte Essen für die Reise.


Odongo ndi Apiyo sibanafune kubwerera ku tauni. Anapempha ambuya awo kuti apitee nawo ku tauni. Koma ambuya anamwetula nati, “Ndine okalamba kwambiri ndipo sindingahkale mu tauni. Ndizayamba kukuyembekeza kuubweranso kwanu kuno kumudzi .”

Als ihr Vater kam, um sie abzuholen, wollten sie nicht gehen. Die Kinder flehten Nyar-Kanyada an, mit ihnen in die Stadt zukommen. Sie lächelte und sagte: „Ich bin zu alt für die Stadt. Ich werde darauf warten, dass ihr wieder zu mir ins Dorf kommt.“


Odongo ndi Apiyo anakumbatirana nao ambuya awo nalayirana .

Odongo und Apiyo umarmten sie fest zum Abschied.


Pamene Odongo nda Apiyo anabwerera kusukulu, anauza anzao za umoyo wakumudzi. Ana ena anadziwa kuti umoyo wa mtauni ndi wabwino. Ena anakonda umoyo wakumudzi. Koma ambiri a iwo, onse ananena kuti ambuya a Odongo ndi Apiyo anali abwino mtima!

Als Odongo und Apiyo wieder in die Schule gingen erzählten sie ihren Freunden vom Dorfleben. Manche Kinder fanden das Leben in der Stadt gut. Aber vor allem waren sich alle einig, dass Odongo und Apiyo eine wundervolle Großmutter hatten!


Geschrieben von: Violet Otieno
Illustriert von: Catherine Groenewald
Übersetzt von: Bether Mwale Moyo
Gelesen von: Christine Mwanza
Sprache: Nyanja
Niveau: Niveau 4
Quelle: Holidays with grandmother aus African Storybook
Creative Commons Lizenz
Dieses Werk ist unter einer Creative Commons Namensnennung 4.0 Lizenz lizenziert.
Optionen
Zurück zur Geschichteliste Schaltfläche PDF