Schaltfläche PDF
Zurück zur Geschichteliste

Simbegwire Simbegwire

Geschrieben von Rukia Nantale

Illustriert von Benjamin Mitchley

Übersetzt von Fredrick Mapulanga

Gelesen von Christine Mwanza

Sprache Nyanja

Niveau Niveau 5

Vollständige Geschichte erzählen Zu dieser Geschichte ist noch kein Audio verfügbar.


Pamene amaiMai a Simbegwire anamwalira, anakhala wacisoni kwambiri. Abambo a Simbegwire adacita zothekera zonse kusamalira mwana wawo wamkazi. Pang’ono-pang’ono, adaphunziranso kusangalalanso, popanda amai a Simbegwire. M’mawa mulimonse amakhala ndikulankhula za tsiku la mawa. Madzulo mulimonse ankadyera pamodzi cakudya camadzulo. Atatsuka mbale, bambo wa Simbegwire anamuthandiza ntchito yasukulu yakunyumba.

Als ihre Mutter starb, war Simbegwire sehr traurig. Simbegwires Vater kümmerte sich so gut er konnte um seine Tochter. Langsam lernten sie, ohne Simbegwires Mutter wieder glücklich zu sein. Jeden Morgen saßen sie zusammen und sprachen über den anstehenden Tag. Jeden Abend bereiteten sie zusammen das Abendessen zu. Nach dem Abwasch half Simbegwires Vater ihr mit den Hausaufgaben.


Tsiku lina, abambo a Simbegwire adafika kunyumba mocedwa kuposa masiku onse. “Kodi mwana wanga uli kuti?” adayitana. Simbegwire anathamangira kwa abambo ake. Anayima pomwe anawona kuti anagwiriradzanja la mkazi. “Ndikufuna iwe ukumane ndi munthu wapadera, mwana wanga. Uyu ndi Anita,” anatero akumwetulira.

Eines Tages kam Simbegwires Vater später als üblich nach Hause. „Wo bist du, mein Kind?“, rief er. Simbegwire lief zu ihm. Sie blieb stehen, als sie sah, dass er die Hand einer Frau hielt. „Ich möchte dir jemand besonderen vorstellen, mein Kind. Das ist Anita“, sagte er lächelnd.


“Moni Simbegwire, abambo ako andiuza zambiri za iwe,” anatero Anita. Koma sanamwetulire kapena kugwirira dzanja la mtsikanayo. Abambo a Simbegwire anali okondwa komanso osangalala. Anakambirana za atatuwa kukhala pamodzi, komanso momwe moyo wawo ungakhalire bwino. “Mwana wanga, ndikhulupirira kuti wavomera Anita kukhala amai ako,” anatero.

„Hallo Simbegwire, dein Vater hat mir viel von dir erzählt“, sagte Anita. Aber weder lächelte sie, noch nahm sie die Hand des Mädchens. Simbegwires Vater war glücklich und erfreut. Er sprach davon, dass die drei zusammenleben und wie schön ihr Leben dann wäre. „Mein Kind, ich hoffe, du akzeptierst Anita als deine Mutter“, sagte er.


Moyo wa Simbegwire unasintha. Sanalinso ndi nthawi yoceza ndi bambo ake m’mawa. Anita anam’patsa ntchito zambiri zapanyumba kotero kuti anali wotopa kwambiri kugwira ntchito yake yakusukulu m’madzulo. Anangopita kukagona atadya cakudya camadzulo. Comwe cinangomutonthoza cinali bulangete wokongola womwe amai ake anampatsa. Abambo a Simbegwire sanadzindikire konse kuti mwana wawo anali wosasangalala.

Simbegwires Leben veränderte sich. Sie hatte keine Zeit mehr, um morgens mit ihrem Vater zu sitzen. Anita gab ihr viel Hausarbeit und abends war sie zu müde von der Schule. Sie ging nach dem Abendessen direkt ins Bett. Der einzige Trost war die bunte Decke, die sie von ihrer Mutter hatte. Simbegwires Vater schien nicht zu bemerken, dass seine Tochter unglücklich war.


Patapita miyezi yaing’ono, abambo a Simbegwire anafotokoza kuti adzacokapo nyumba kwakanthawi. “Ndiyenera kupita kuntchito yanga,” adatero. “Koma ndikudziwa mudzasamalirana.” Nkhope ya Simbegwire idagwa, koma abambo ake sanazindikire konse. Anita sananene ciriconse. Sanasangalale nayenso.

Nach ein paar Monaten, teilte Simbegwires Vater ihnen mit, dass er eine Weile nicht zu Hause sein würde. „Ich muss von meiner Arbeit aus verreisen“, sagte er. „Aber ich weiß, dass ihr auf euch gegenseitig aufpasst.“ Simbegwire schaute betrübt, aber ihr Vater bemerkte es nicht. Anita sagte nichts. Auch sie war nicht glücklich.


Zinthu zinafika poipa kwa Simbegwire. Ngati sanamalize ntchito zake, kapena kumadandaula, Anita amamumenya. Ndipo pacakudya camadzulo, maiyo amadya cakudya cambiri, nasiyira Simbegwire zidutswa zocepa cabe. Usiku uliwonse Simbegwire amalira yekha kugona, kukumbatira bulangete wa amai ake.

Es wurde schlimmer für Simbegwire. Wenn sie ihre Aufgaben nicht erledigte oder sie sich beschwerte, schlug Anita sie. Und beim Abendessen aß die Frau das meiste Essen, sodass für Simbegwire nur einige Reste übrig blieben. Jeden Abend weinte sich Simbegwire mit der Decke ihrer Mutter im Arm in den Schlaf.


Tsiku lina m’mawa, Simbegwire anacedwa kuuka. “Iwe mwana waulesi!” Anita anafuula. Anamcotsa Simbegwire pabedi. Bulangete wamtengo wapatali anagwidwa ndi msomali, ndipo unang’ambika pakati.

Eines Morgens stand Simbegwire zu spät auf. „Du faules Mädchen!“, rief Anita. Sie zog Simbegwire aus dem Bett. Die Lieblingsdecke blieb an einem Nagel hängen und riss entzwei.


Simbegwire anakhumudwa kwambiri. Anaganiza zothawa kucoka panyumba. Anatenga zidutswa za bulangete wa amai ake, nanyamula cakudya, natuluka mnyumbamo. Anatsatira njira yomwe abambo ake anapitira.

Simbegwire war sehr verärgert. Sie beschloss, von zu Hause wegzulaufen. Sie nahm die zerrissene Decke ihrer Mutter, packte etwas zu essen ein und verließ das Haus. Sie lief den Weg entlang, den ihr Vater genommen hatte.


Pofika madzulo, anakwera mtengo wautali pafupi ndi mtsinje ndipo anadzipangira pogona panthambi. Pomwe anagona, anayimba: Maama, maama, maama, munandisiya. Munandisiya osabweranso. Atate sakundikondanso. Amai, mudzabwera liti? Munandisiya.”

Als es Abend wurde kletterte sie auf einen hohen Baum nahe des Flusses und machte sich ein Bett in den Ästen. Zum Einschlafen sang sie: „Maama, Maama, Maama, du hast mich verlassen. Du hast mich verlassen und bist nie zurückgekommen. Vater liebt mich nicht mehr. Mutter, wann kommst du zurück? Du hast mich verlassen.“


M’mawa mwake, Simbegwire anayimbanso nyimboyo. Pomwe azimaimai anabwera kudzachapa zovala zawo pamtsinje, anamva nyimbo yacisoni ikucokera mumtengo wautali. Amaganiza kuti ndi mphepo yomwe imawaza masamba, ndikupitirira ndi ntchito yawo. Koma m’modzi mwa azimaiwo anamvetsera mosamalitsa ku nyimboyi.

Am nächsten Morgen sang Simbegwire wieder das Lieb. Als die Frauen zum Fluss kamen, um ihre Kleidung zu waschen, hörten sie das traurige Lied aus dem großen Baum kommen. Sie dachten, es sei nur der Wind, der in den Blättern raschelte und setzten ihre Arbeit fort. Aber eine der Frauen hörte dem Lied ganz genau zu.


Mai uyu anayang’ana m’mtengo. Ataona mtsikanayo ndi zidutswa za bulangete wokongola, aafuula, “Simbegwire, mwana wa mcimwene wanga!” Amai enawo anasiya kutsuka ndikuthandizira Simbegwire kutsika m’mtengo. Azakhali ake anakumbatira kamtsikanaka ndikuyesetsa kumutonthoza.

Die Frau schaute hinauf in den Baum. Als sie das Mädchen und Teile der bunten Decke sah, rief sie „Simbegwire, das Kind meines Bruders!“ Die anderen Frauen unterbrachen das Waschen und halfen Simbegwire, den Baum hinunter zu klettern. Ihre Tante umarmte das kleine Mädchen und versuchte, es zu trösten.


Azakhali ake a Simbegwire adapita ndi mwana kunyumba kwake. Anapatsa Simbegwire cakudya cothuma, ndikumugoneka pabedi ndi bulangete wa amai ake. Usiku womwewo, Simbegwire analira pamene anali kugona. Koma inali misozi yampumulo. Anadziwa kuti azakhali ake azamusamalira.

Simbegwires Tante nahm das Kind mit zu sich nach Hause. Sie gab Simbegwire eine warme Mahlzeit und deckte sie im Bett mit der Decke ihrer Mutter zu. In dieser Nacht weinte sich Simbegwire in den Schlaf, aber es waren Tränen der Erleichterung. Sie wusste, ihre Tante würde sich um sie kümmern.


Pamene abambo a Simbegwire atabwelerako, anapeza cipinda cake ciribe kanthu. “Cinacitika ndi ciani, Anita?” anafunsa ndi mtima wokhumudwa. Maiyo analongosola kuti Simbegwire anathawa. “Ndidafuna kuti iye andiremekeze,” anatero. “Koma mwina ndinali okhwimitsa zinthu.” Abambo a Simbegwire anacoka mnyumbamo ndi kulowera ca kumtsinje. Adapitirizabe kupita kumudzi kwa mlongo wake kuti akafunse ngati anamuonako Simbegwire.

Als Simbegwires Vater nach Hause kam, fand er ein leeres Zimmer vor. „Was ist passiert, Anita?“ fragte er traurig. Die Frau erklärte, dass Simbegwire weggelaufen war. „Ich wollte, dass sie mich respektiert“, sagte sie, „aber vielleicht war ich zu streng.“ Simbegwires Vater ging hinaus und lief in Richtung Fluss. Er lief zum Dorf seiner Schwester, um herauszufinden, ob sie Simbegwire gesehen hatte.


Simbegwire anali kusewera ndi azisuweni ake ataona bambo wake kutali. Anacita mantha kuti mwina adzakwiya, motero anathamangira mnyumba kukabisala. Koma abambo ake anapita kwa iye nati, “Simbegwire, wadzipezera wekha mai wako wabwinomai. Yemwe akukonda ndikukumvetsetsa. Ndikunyadira ndipo ndikukonda.” Anagwirizana kuti Simbegwire azikhala ndi azakhali ake kulingana ndi momwe angafunire.

Simbegwire spielte mit ihren Cousins als sie ihren Vater von weit weg kommen sah. Sie hatte Angst, dass er wütend sein könnte, also lief sie ins Haus, um sich zu verstecken. Aber ihr Vater sagte: „Simbegwire, du hast dir selbst eine perfekt Mutter gesucht. Eine, die dich liebt und versteht. Ich bin stolz auf dich und ich liebe dich.“ Sie vereinbarten, dass Simbegwire so lange bei ihrer Tante bleiben würde, wie sie möchte.


Abambo ake amamuyendera tsiku lirironse. Pambuyo pake, anabwera ndi Anita. Anatambasulira dzanja lake kwa Simbegwire. “Pepani, ndinalakwitsa,” analira. “Kodi ungandirole kuyesanso?” Simbegwire anayang’ana abambo ake ndi nkhope yawo ya nkhawa. Kenako anayenda pang’onopang’ono cakutsogolo ndikukumbatira Anita.

Ihr Vater kam jeden Tag zu Besuch. Irgendwann kam er zusammen mit Anita. Sie nahm Simbegwires Hand. „Es tut mir so leid, Kleine, es war mein Fehler“, weinte sie. „Kannst du mir noch eine Chance geben?“ Simbegwire sah ihren besorgten Vater an. Dann machte sie einen Schritt auf Anita zu und legte ihren Arm um sie.


Sabata yotsatira, Anita adayitanitsa Simbegwire, ndi abale ake ndi azakhali ake, kunyumba kuti akadye. Ndi phwando labwino bwanji! Anita anakonza zakudya zonse zomwe Simbegwire amakonda, ndipo aliyense anadya mpaka atakhuta. Kenako ana anasewera pomwe akulu amalankhula. Simbegwire anali wosangalala komanso wolimba mtima. Anaganiza kuti posachedwa, abwerera kunyumba kukakhala ndi abambo ndi amai ake omupeza.

In der Woche danach lud Anita Simbegwire mit ihren Cousins und der Tante zum Essen ein. Was für ein Fest! Anita kochte Simbegwires Lieblingsessen und alle aßen, bis sie satt waren. Dann spielten die Kinder, während die Erwachsenen sich unterhielten. Simbegwire war glücklich und tapfer. Sie beschloss, dass sie bald, sehr bald, zurück nach Hause kommen würde, um bei ihrem Vater und ihrer Stiefmutter zu wohnen.


Geschrieben von: Rukia Nantale
Illustriert von: Benjamin Mitchley
Übersetzt von: Fredrick Mapulanga
Gelesen von: Christine Mwanza
Sprache: Nyanja
Niveau: Niveau 5
Quelle: Simbegwire aus African Storybook
Creative Commons Lizenz
Dieses Werk ist unter einer Creative Commons Namensnennung 3.0 Lizenz lizenziert.
Weitere Niveau 5 Geschichten lesen:
Optionen
Zurück zur Geschichteliste Schaltfläche PDF