返回故事列表
Simbegwire
辛波薇亚
Rukia Nantale
Benjamin Mitchley
Fredrick Mapulanga
Christine Mwanza
本故事尚未有语音版。
Pamene amai a Simbegwire anamwalila, anakhala wacisoni kwambili. Abambo a Simbegwire adacita zothekela zonse kusamalila mwana wawo wamkazi. Pang’ono-pang’ono, adaphunzilanso kusangalalanso, popanda amai a Simbegwire. M’mawa mulimonse amakhala ndikulankhula za tsiku la mawa. Madzulo mulimonse ankadyela pamodzi cakudya camadzulo. Atatsuka mbale, bambo wa Simbegwire anamuthandiza ntchito yasukulu yakunyumba.
辛波薇亚的妈妈过世的时候,她非常伤心。辛波薇亚的爸爸尽全力照顾孩子。时间久了,他们渐渐开心起来,习惯了没有辛波薇亚妈妈的生活。每天早上,他们坐在一起,谈论着即将到来的一天。每天晚上,他们一起做饭,然后一起洗碗,辛波薇亚的爸爸还帮助她做功课。
Tsiku lina, abambo a Simbegwire adafika kunyumba mocedwa kuposa masiku onse. “Kodi mwana wanga uli kuti?” adayitana. Simbegwire anathamangila kwa abambo ake. Anayima pomwe anawona kuti anagwilila dzanja la mkazi. “Ndikufuna iwe ukumane ndi munthu wapadela, mwana wanga. Uyu ndi Anita,” anatelo akumwetulila.
有一天,辛波薇亚的爸爸回家晚了。他一进门就喊道:“亲爱的孩子,你在哪里?”辛波薇亚跑出来迎接爸爸。但她突然停住了,因为她看到爸爸牵着另外一个女人的手。爸爸笑着说:“我的孩子,来,我向你介绍一个很特别的人,她叫阿妮塔。”
“Moni Simbegwire, abambo ako andiuza zambili za iwe,” anatelo Anita. Koma sanamwetulile kapena kugwilila dzanja la mtsikanayo. Abambo a Simbegwire anali okondwa komanso osangalala. Anakambilana za atatuwa kukhala pamodzi, komanso momwe moyo wawo ungakhalile bwino. “Mwana wanga, ndikhulupilila kuti wavomela Anita kukhala amai ako,” anatelo.
阿妮塔跟辛波薇亚打招呼:“你好,辛波薇亚!你的爸爸跟我说了很多关于你的事。”她没有朝辛波薇亚微笑,也没有牵她的手。辛波薇亚的爸爸很高兴,他兴奋地说着,如果他们三个人住在一起,一定会很幸福的。爸爸朝辛波薇亚说:“我的孩子,我希望你能接受阿妮塔成为你的母亲。”
Moyo wa Simbegwire unasintha. Sanalinso ndi nthawi yoceza ndi bambo ake m’mawa. Anita anam’patsa ntchito zambili zapanyumba kotelo kuti anali wotopa kwambili kugwila ntchito yake yakusukulu m’madzulo. Anangopita kukagona atadya cakudya camadzulo. Comwe cinangomutonthoza cinali bulangete wokongola womwe amai ake anampatsa. Abambo a Simbegwire sanadzindikile konse kuti mwana wawo anali wosasangalala.
辛波薇亚的生活变了。她每天早上没有时间和爸爸坐在一起聊天。阿妮塔让辛波薇亚做很多家务,辛波薇亚每天晚上都累极了,根本没有时间做功课。她一吃完晚饭就睡觉了。她唯一的安慰就是妈妈留给她的彩色毯子。辛波薇亚的爸爸似乎没有意识到女儿一点儿也不开心。
Patapita miyezi yaing’ono, abambo a Simbegwire anafotokoza kuti adzacokapo pa nyumba kwakanthawi. “Ndiyenela kupita kuntchito yanga,” adatelo. “Koma ndikudziwa mudzasamalilana.” Nkhope ya Simbegwire idagwa, koma abambo ake sanazindikile konse. Anita sananene ciliconse. Sanasangalale nayenso.
过了几个月,辛波薇亚的爸爸告诉她们,他要离家一段时间。他说:“我得出差,我相信你们会互相照顾对方的。”辛波薇亚低下头,但她的爸爸没有注意。阿妮塔什么也没说,她也不太高兴。
Zinthu zinafika poipa kwa Simbegwire. Ngati sanamalize ntchito zake, kapena kumadandaula, Anita amamumenya. Ndipo pacakudya camadzulo, maiyo amadya cakudya cambili, nasiyila Simbegwire zidutswa zocepa cabe. Usiku uliwonse Simbegwire amalila yekha kugona, kukumbatila bulangete wa amai ake.
辛波薇亚的生活变得更糟糕了。如果辛波薇亚没有做完家务,或者她稍微有点抱怨的话,阿妮塔就会打她。晚上,阿妮塔把大多数食物都吃了,只留给辛波薇亚一点剩饭剩菜。每天晚上,辛波薇亚都流着泪入睡,她只能紧紧地抱着妈妈留下的毯子。
Tsiku lina m’mawa, Simbegwire anacedwa kuuka. “Iwe mwana waulesi!” Anita anafuula. Anamcotsa Simbegwire pabedi. Bulangete wamtengo wapatali anagwidwa ndi msomali, ndipo unang’ambika pakati.
一天早上,辛波薇亚起床晚了。阿妮塔气极了:“你这个懒虫!”她把辛波薇亚从床上拉起来。毯子勾到一颗钉子,撕成了两半。
Simbegwire anakhumudwa kwambili. Anaganiza zothawa kucoka panyumba. Anatenga zidutswa za bulangete wa amai ake, nanyamula cakudya, natuluka mnyumbamo. Anatsatila njila yomwe abambo ake anapitila.
辛波薇亚伤心透了,她决定离家出走。她带着毯子的碎片,包了一些食物,沿着爸爸出差的路离开了家里。
Pofika madzulo, anakwela mtengo wautali pafupi ndi mtsinje ndipo anadzipangila pogona panthambi. Pomwe anagona, anayimba: Maama, maama, maama, munandisiya. Munandisiya osabwelanso. Atate sakundikondanso. Amai, mudzabwela liti? Munandisiya.”
天黑了,辛波薇亚找到一棵长在小溪旁边的树。她爬上了树,在树枝上搭了一张小床。她唱着歌,渐渐睡着了:“妈妈,妈妈,妈妈,你离开了我,离开了我再也不回来了。爸爸再也不爱我了。妈妈,你什么时候回来,你离开了我……”
M’mawa mwake, Simbegwire anayimbanso nyimboyo. Pomwe azimaimai anabwela kudzachapa zovala zawo pamtsinje, anamva nyimbo yacisoni ikucokela mumtengo wautali. Amaganiza kuti ndi mphepo yomwe imawaza masamba, ndikupitilila ndi ntchito yawo. Koma m’modzi mwa azimaiwo anamvetsela mosamalitsa ku nyimboyi.
第二天早上,辛波薇亚又唱起了这首歌。附近的女人到溪水边来洗衣服,她们听到了树上传来的歌声。她们以为这是风穿过树叶的声音,于是就没有在意,继续洗衣服。但其中有个女人仔细地听着这首歌。
Mai uyu anayang’ana m’mtengo. Ataona mtsikanayo ndi zidutswa za bulangete wokongola, aafuula, “Simbegwire, mwana wa mcimwene wanga!” Amai enawo anasiya kutsuka ndikuthandizila Simbegwire kutsika m’mtengo. Azakhali ake anakumbatila kamtsikanaka ndikuyesetsa kumutonthoza.
女人抬起头来看着那棵树。当她看到辛波薇亚和那条彩色的毯子时,她吓了一跳:“辛波薇亚,我哥哥的孩子!”其他的女人也停下了手里的活儿,帮助辛波薇亚从树上爬了下来。她的姑姑紧紧地抱着她,尽量安慰她。
Azakhali ake a Simbegwire adapita ndi mwana kunyumba kwake. Anapatsa Simbegwire cakudya cothuma, ndikumugoneka pabedi ndi bulangete wa amai ake. Usiku womwewo, Simbegwire analila pamene anali kugona. Koma inali misozi yampumulo. Anadziwa kuti azakhali ake azamusamalila.
辛波薇亚的姑姑带着她去了自己家。她给辛波薇亚煮了美味的食物,又给她铺了床,让她盖着妈妈的毯子睡觉。那天晚上,辛波薇亚又哭着睡着了。不过这次是欣慰的泪水。她知道她的姑姑会照顾她。
Pamene abambo a Simbegwire atabwelelako, anapeza cipinda cake cilibe kanthu. “Cinacitika ndi ciani, Anita?” anafunsa ndi mtima wokhumudwa. Maiyo analongosola kuti Simbegwire anathawa. “Ndidafuna kuti iye andilemekeze,” anatelo. “Koma mwina ndinali okhwimitsa zinthu.” Abambo a Simbegwire anacoka mnyumbamo ndi kulowela ca kumtsinje. Adapitilizabe kupita kumudzi kwa mlongo wake kuti akafunse ngati anamuonako Simbegwire.
辛波薇亚的爸爸回到家里,发现辛波薇亚的房间里空荡荡的。他疲倦极了,问阿妮塔发生了什么事。阿妮塔说辛波薇亚离家出走了。她解释道:“我只是想让她尊敬我,但是我可能太严格了。”辛波薇亚的爸爸跑出家门,沿着小溪去找辛波薇亚。他走到了妹妹的村庄,想问问她有没有见过辛波薇亚。
Simbegwire anali kusewela ndi azisuweni ake ataona bambo wake kutali. Anacita mantha kuti mwina adzakwiya, motelo anathamangila mnyumba kukabisala. Koma abambo ake anapita kwa iye nati, “Simbegwire, wadzipezela wekha mai wako wabwino mai. Yemwe akukonda ndikukumvetsetsa. Ndikunyadila ndipo ndikukonda.” Anagwilizana kuti Simbegwire azikhala ndi azakhali ake kulingana ndi momwe angafunile.
辛波薇亚正在和她的表兄弟姐妹玩耍,但她突然看到了远处的爸爸。她害怕爸爸会生气,于是就跑到房子里躲了起来。但是爸爸找到她,对她说:“辛波薇亚,你自己找到了一个完美的妈妈,她爱你,理解你。我为你感到骄傲,我爱你。”他们商量后决定辛波薇亚可以和姑姑住在一起,想呆多久就可以呆多久。
Abambo ake amamuyendela tsiku lililonse. Pambuyo pake, anabwela ndi Anita. Anatambasulila dzanja lake kwa Simbegwire. “Pepani, ndinalakwitsa,” analila. “Kodi ungandilole kuyesanso?” Simbegwire anayang’ana abambo ake ndi nkhope yawo ya nkhawa. Kenako anayenda pang’ono pang’ono cakutsogolo ndikukumbatila Anita.
辛波薇亚的爸爸每天都来看她。有一天,他和阿妮塔一起来了。阿妮塔朝辛波薇亚伸出手,她哭了:“我太抱歉了,小家伙,对不起,我错了,你可以再给我一次机会吗?”辛波薇亚看了看爸爸,看到他忧虑的脸庞。她朝前走了一步,抱住了阿妮塔。
Sabata yotsatila, Anita adayitanitsa Simbegwire, ndi abale ake ndi azakhali ake, kunyumba kuti akadye. Ndi phwando labwino bwanji! Anita anakonza zakudya zonse zomwe Simbegwire amakonda, ndipo aliyense anadya mpaka atakhuta. Kenako ana anasewela pomwe akulu amalankhula. Simbegwire anali wosangalala komanso wolimba mtima. Anaganiza kuti posachedwa, abwelela kunyumba kukakhala ndi abambo ndi amai ake omupeza.
过了几天,阿妮塔邀请辛波薇亚,姑姑和姑姑的孩子们一起到家里吃饭。好丰盛啊!而且那都是辛波薇亚喜欢吃的东西,每个人都吃得津津有味。吃完饭,大人们在家里聊天,孩子们在外面玩耍。辛波薇亚觉得很开心,自己变得更加勇敢了。她决定不久以后就要回到家里,和自己的爸爸,继母住在一起。
作者: Rukia Nantale
插图: Benjamin Mitchley
译文: Fredrick Mapulanga
配音: Christine Mwanza