下载 PDF
返回故事列表

Magozwe 玛格威

作者 Lesley Koyi

插图 Wiehan de Jager

译文 Bether Mwale Moyo

配音 Christine Mwanza

语言 齐切瓦语

级别 5级

将整故事念出来 本故事尚未有语音版。


Mu tauni ya Nairobi, kutali nama banja, kunali kunkala anyamata analibe mabanja. Anangonkala mwa siku pa siku. Kuseni kwina, anyamata anali kulonga mpasa zao pambuyo pogona pampepo mumbali mwa museu. Kusewenzesa vinyalala, anayasa moto kuti asangenewe mpepo. Pagulu la anyamata ili panali Magozwe. Iye ndiye anali wamung’ono.

在内罗毕这座繁忙的城市里,住着一群流浪的男孩,他们日复一日地活着,从来不知道什么是舒适安逸的生活。一天早上,男孩们从冰冷的人行道上醒来,把他们用来睡觉的毯子叠起来。天太冷了,为了驱赶寒气,他们用拾来的垃圾燃起了一堆火。在这群男孩中有一个人叫玛格威。


Pomwe makolo ake Magozwe anamwalila, iye anali na zaka cabe kumi. Ndipo anayenda kunkala na amalume ake. Amalume ake sanatayeko nzelu kwa mwana. Sanali kumupasa cakudwa cokwanila Magozwe. Ndipo anali kugwilisa ncito zambili.

玛格威的父母过世时,他只有五岁,他搬去跟叔叔一起生活。叔叔从来不关心玛格威。玛格威在叔叔家挨饿受冻,还要干很多体力活。


Ngati Magozwe wafunsa mwina wadandaula, amalume ake anali kumumenya. Pomwe anafunsa kuti ayende kusukulu amalume ake anamumenya nanena nati “Ndiwe cisilu kwambili sungapunzile kalikonse.” Patapita zaka zitatu zosungiwa mozuzindwa, Magozwe anataba kucoka pa nyumba pa amalume ake. Ndipo anayamba kunkala pa museu.

一旦玛格威稍有抱怨,叔叔就会对他拳打脚踢。有一次,玛格威问叔叔他能不能去上学,叔叔狠狠地打了他几下,说:“你这傻瓜,用得着上学吗?”玛格威过了三年这样的日子,终于离家出走,无家可归。


Kunali kovuta kunkala kwa pa museu ndipo anyamata ambili anali kuvutika masiku onse kupeza cakudya. Masiku ena anamenyedwa, ntawi zina anagwilidwa na apolisi. Akadwala kunalibe muntu owatandiza. Ndalama zomwe anapeza mukupempa pempa, kugulisa ma pulasitiki na zina, ndiye ndalama zomwe zinali kuwatandizila. Umoyo unavutilako cifukwa magulu ena a anyamata anali kufuna kulanda malo osiyana siyana mu tauni.

流浪生活非常艰辛,大多数男孩每天只能混个温饱。他们有时候会被抓起来,有时候会挨打。当他们生病的时候,没有人照顾他们。这群男孩就靠乞讨得来的一点点钱过活,他们有时候也会卖塑料品和旧货赚点钱。有时候别的流浪汉会来找茬,争夺领地,那时候生活就更艰难。


Siku lina pamene Magozwe anali kusakila-sakila muvinyalala, anapeza buku lina losila long’ambika. Anacosako madoti ndipo analiika mu saka. Siku lililonse lokonkapo, anacosa buku ndipo anayamba kulangana vitunzi tunzi mu buku. Sanali kuziwa kuwelenga mau.

有一天,玛格威正在翻垃圾箱,他找到了一本破旧不堪的故事书。他把书上的灰尘吹走,把书放进了袋子里。每天完工后,他会把书拿出来,翻着上面的图画,可惜他看不懂上面的文字。


Vitunzi tunzi vinalangiza munyamata omwe anakula kunkala oyendesa ndeke. Magozwe analota na muzuba momwe, kunkala oyendesa ndeke. Ntawi zina anaziona kuti ndiye wamene anali munyamata wamubuku.

图画书讲的是一个男孩长大成为飞行员的故事。玛格威有时候会梦想自己成为一个飞行员。有时候,他想象着自己就是故事中的男孩。


Kunali kozizila ndipo Magozwe anaimilila pa museu kupempa-pempa. Muzibambo wina anabwela pafupi naye. “Bwanji, ndine Thomas. Nisewenza pafupa napano, pamalo pamene ungapeze cakudya,” anakamba. Anasonta nyumba yacikasu, ya malata yobilibila. “Niziwa uzayenda kuti utengeko cakudya?” anafunsa. Magozwe analangana muzibambo nalangana nyumba. “Kapena nizayenda,” anayanka, ndipo anacokapo.

有一天,天气很冷,玛格威站在街头乞讨。一个男人走过来,跟他打招呼:“你好,我叫托马斯。我在这儿附近工作,你可以到那儿拿点吃的。”他指着一座蓝顶黄墙的房子,“我希望你别客气,到那儿去拿点吃的吧!”玛格威看了看男人,又看了看房子,说:“可能吧!”然后他就走开了。


Panapita Mwezi, ndipo anyamata alibe mabanja anali kuonana na Thomas. Thomas anali kukonda kukamba na antu makamaka antu onkala pa museu. Thomas ananvesela nkani za antu awa. Anali wacidwi ndipo wonkazikika mutima, ndiponso sanataye ulemu. Anyamata ena anayamba kuyenda kunyumba yacikasu ya malata obilibila, kutenga cakudya muzuba.

接下来的几个月,流浪的男孩们渐渐认识了托马斯。他喜欢跟人聊天,特别是无家可归的人。托马斯听别人讲他们的故事。他不苟言笑,非常耐心、有礼貌,尊重他人。一些男孩开始在白天去蓝顶黄墙的房子里找吃的。


Magozwe anali nkale mumbali mwa museu alangana vitunzi tunzi mu buku yake pamene Thomas anabwela nankala pafupi naye. “Ikamba cani nkani?” anafunsa Thomas. “Ikamba pali munyamata amena anankala oyendesa ndeke,” anayanka Magozwe. “Nindani zina munyamata?” anafunsa Thomas. “Kaya, siniziba kuwelenga,” anayanka Magozwe mwacisinsi.

有一天,玛格威正坐在人行道上看故事书,托马斯来了坐在他旁边。托马斯问:“这本书讲了什么故事?”玛格威回答说:“这是关于一个男孩成为飞行员的故事。”托马斯问:“男孩叫什么名字?”玛格威声音低了下去:“我不知道,我不识字。”


Pomwe anakumana, Magozwe anayamba kuuza Thomas, nkani za umoyo wake. Anamuuza za mwamene anatawila kucoka kwa amalume ake. Thomas sanakambe kwambili, ndipo sanauze Magozwe vocita koma anamvesela mwacidwi. Ntawi zina Magozwe na Thomas anakambilana pamene anali kudya munyumba ya malata obilibila.

当他们再次见面的时候,玛格威开始跟托马斯讲自己的故事,他的叔叔怎么对他,他怎么逃离了叔叔家。托马斯没说什么,也没有告诉玛格威该怎么做,但是他听得很仔细。有时候他们会一边在蓝顶黄墙的房子里吃东西,一边聊聊天。


Pomwe Magozwe anali pafupi nakukwanisa zaka kumi, Thomas anamupasa buku. Buku inali pali munyamata wa mumunzi wamene anakula kunkala womenya bola wozibika kwambili. Thomas anamuwelengela Magozwi kwambili, mpaka siku lina anakamba nati, “Niganiza kuti uyambe kuyenda ku sukulu, kuti ukapunzile kuwelenga. Uganizapo bwanji?” Thomas anakamba kuti anali kuziba malo kumene ana angayende kunkala ndiponso kupunzila kwameneko.

玛格威十岁生日的时候,托马斯给了他一本新的故事书,这是关于一个乡下男孩成为足球运动员的故事。托马斯给玛格威讲过这个故事很多次。有一天,托马斯说:“我觉得你应该去上学,去识字。你觉得呢?”托马斯说他知道一个地方,孩子们可以住在那儿,上学。


Magozwe anaganizila za kumalo uko ndiponse zoyenda ku sukulu. Nanga kapena amalume ake anakamba zoona kuti anali cisilu kwambili ndipo sangapunzile kalikonse? Nanga ngati bamumenya uku kumalo kwinangu? Anayopa. “Kapena cilibwino kupitiliza kunkala pa museu,” anaganiza.

玛格威想了想去新地方生活,上学。但是,如果他叔叔说得对,他太笨了上不了学怎么办?如果在新的地方,他又要挨打怎么办?他有点儿害怕,心想:“也许我注定就要睡在马路边。”


Anamuuza Thomas kuti anali na manta. Thomas anamusimikizila kuti, azankala na umoyo wabwina uku kumalo.

他把自己的想法告诉了托马斯。托马斯对他循循善诱,终于说服了玛格威,他在新地方一定会过上更好的生活。


Ndipo Magozwe anapita kunkala mu cipinda mu nyumba ya malata amusipu. Anankala na anyamata ena awili mu cipinda. Pamozi anali anyamata kumi amene anali kunkala pamozi mu nyumba. Pamozi na a Anti Cissy na amuna ao, magalu atatu, ka kiti na mbuzi yokalamba.

玛格威搬到了新家,新家的屋顶是绿色的。他和两个男孩住一间房间。屋子里还住着其他十个孩子。和他们住在一起的是茜茜阿姨和她的丈夫,还有三只狗,一只猫,一头老山羊。


Magozwe anayamba sukulu ndipo inali yovuta. Nivambili vamene anali kufunikila kuziwa kuti alingane na anzake. Ntawi zina anali kufuna kuleka. Koma anaganizila oyendesa ndeke na omenya bola a muma buku ake. Monga aja anyamata amumabuku, sanaleke.

玛格威开始读书,他遇到了不少困难,很难赶上他的同学们,有时候他差点就要放弃了。但他每次想起故事书里的飞行员和足球运动员,他都坚持了下来,就像他们一样。


Magozwe anali nkale panja panyumba ya malata a musipu, awelenga buku lake lakusukulu, pamene Thomas anabwela nonkala pafupi pake. “Ikamba cani nkani?” anafunsa Thomas. “Ikamba pali munyamata amene anankala mupunzisi,” anayanka Magozwe. “Nindani zina munyamata?” anafunsa Thomas. “Zina lake ni Magozwe,” anayanka Magozwe mosekelela.

有一天,玛格威正在屋子后院里看书,托马斯来了,坐在他旁边:“这本书讲了什么故事?”玛格威回答说:“这是关于一个男孩变成老师的故事。”托马斯问:“那个男孩叫什么名字?”玛格威咧嘴一笑:“他叫玛格威。”


作者: Lesley Koyi
插图: Wiehan de Jager
译文: Bether Mwale Moyo
配音: Christine Mwanza
语言: 齐切瓦语
级别: 5级
出处: 原文来自非洲故事书Magozwe
共享创意授权条款
本着作系采用共享创意 署名 4.0 未本地化版本授权条款授权。
读多啲5级故事:
选项
返回故事列表 下载 PDF