Njovu imozi iyenda kukamwa madzi
One elephant is going to drink water.
Un éléphant va boire de l’eau.
Anyamalikiti awiri ayenda kukamwa madzi
Two giraffes are going to drink water.
Deux girafes vont boire de l’eau.
Njati zitatu ndi mbalame zinai nazonso ziyenda kukamwa madzi
Three buffaloes and four birds are also going to drink water.
Trois bœufs et quatre oiseaux vont boire de l’eau.
Mphala zisanu ndi nkhumba zakuchile zisanu ndi imozi zipita kumadzi
Five impalas and six warthogs are walking to the water.
Cinq impalas et six phacochères vont boire de l’eau.
Mbizi zisanu ndi ziwiri zithamangila kumadzi
Seven zebras are running to the water.
Sept zèbres courent vers l’eau.
Acule asanu ndi atatu kuzanso nsomba zisanu ndi zinai zinyaya m’madzi
Eight frogs and nine fish are swimming in the water.
Huit grenouilles et neuf poissons nagent dans l’eau.
Mkango umozi walira. Afunanso kumwa madzi. Ndani amene aopa mkango?
One lion roars. He also wants to drink. Who is afraid of the lion?
Un lion rugit. Il veut boire aussi. Qui a peur du lion ?
Njovu imozi ikumwa madzi ndi mkango
One elephant is drinking water with the lion.
Un éléphant boit de l’eau avec le lion.