Njovu imozi ipita kukamwa madzi.
Un elefante va a beber agua.
Anyamalikiti awili apita kukamwa madzi.
Dos jirafas van a beber agua.
Njati zitatu ndi mbalame zinai nazonso zipita kukamwa madzi.
Tres búfalos y cuatro pájaros también van a beber agua.
Mphala zisanu ndi nguluwe zisanu ndi imozi zipita kumadzi.
Cinco impalas y seis jabalíes están caminando hacia el agua.
Mbizi zisanu ndi ziwili zithamangila kumadzi.
Siete cebras están corriendo hacia el agua.
Acule asanu ndi atatu kudzanso nsomba zisanu ndi zinai zinyaya m’madzi.
Ocho ranas y nueve peces están nadando en el agua.
Mkango umozi walila. Afunanso kumwa madzi. Ndani amene aopa mkango?
Un león ruge. También quiere beber. ¿Quién le tiene miedo al león?
Njovu imozi ikumwa madzi ndi mkango.
Un elefante está bebiendo agua con el león.