Retour à la liste des contes
Ganizo
La décision
Ursula Nafula
Vusi Malindi
David Sani Mwanza
Christine Mwanza
L’enregistrement audio de cette histoire est actuellement indisponible.
Mudzi wanga unali ndi mabvuto ambili. Timaima m’mzele wautali umodzi kutunga madzi pa pompi imodzi.
Mon village avait beaucoup de problèmes. Nous faisions la queue pour aller chercher de l’eau d’un seul robinet.
Tinayembekezela zakudya zopelekedwa ndi ena.
Nous attendions la nourriture donnée par les autres.
Tinakhoma manyumba athu mwamsanga cifukwa coopa akawalala.
Nous barrions nos maisons tôt à cause des voleurs.
Ana ambili analeka sukulu.
Plusieurs enfants avaient abandonné l’école.
Atsikana ang’ono ang’ono anasewenza maganyu m’midzi ina.
Les jeunes filles travaillaient comme domestiques dans d’autres villages.
Anyamata ang’ono ang’ono anali kuyendayenda m’midzi ina ndipo ena anali kuchita ganyu m’minda ya ena.
Les jeunes garçons se promenaient autour du village pendant que d’autres travaillaient sur des fermes.
Pamene mphepo ikuntha, mapepala opanda nchito anapacikika pa mitengo ndi mipanda.
Quand le vent soufflait, des déchets de papier pendaient des arbres et des clôtures.
Anthu anacekedwa ndi magalasi oonongeka amane anataidwa mosasamala.
Les gens se faisaient couper par de la vitre brisée lancée sans faire attention.
Ndipo tsiku lina, pompi inauma ndipo migomo yathu inalibe madzi.
Puis un jour, le robinet se tarit et nos conteneurs étaient vides.
Atate anga anayenda khomo ndi khomo kupempha anthu kuti apite ku msonkhano wa m’mudzi.
Mon père marcha de maison en maison et demanda aux gens de participer à une réunion du village.
Anthu anasonkhana pansi pa mtengo ukulu ndipo anamvesela.
Les gens se rassemblèrent sous un grand arbre et écoutèrent.
Atate anga anaima nati, “Tifunika kusewenzela pamozi kuti tithetse mabvuto athu.”
Mon père se leva et dit, « Nous devons travailler ensemble pour résoudre nos problèmes. »
Juma wa zaka zisanu ndi zitatu, omwe anakhala pa nthambi ya mtengo anakuwa nati “Ndingathandize ndi kusesa.”
Juma, âgée de huit ans et assise sur un tronc d’arbre, cria, « Je peux aider à nettoyer. »
Mai m’mozi anati “azimai angasewenze pamozi ndi ine kuti tilime zakudya.”
Une femme dit, « Les femmes peuvent me joindre pour faire pousser de la nourriture. »
Bambo wina anaimilila nati “Amuna azakumba citsime.”
Un autre homme se leva et dit, « Les hommes creuseront un puits. »
Tonse tinakuwa ndi mau amozi ndikuti, “tifunika kusintha myoyo yathu.” Kucoka pa tsiku lija, tinasewenzela pamozi kuthetsa mabvuto athu.
Nous criions tous d’une seule voix, « Nous devons changer nos vies. » Depuis ce jour, nous avons travaillé ensemble pour résoudre nos problèmes.
Écrit par: Ursula Nafula
Illustré par: Vusi Malindi
Traduit par: David Sani Mwanza
Lu par: Christine Mwanza