Back to stories list
Zama ndi wamphamvu
Zama is great!
Michael Oguttu
Vusi Malindi
Jessy Sakala
The audio for this story is currently not available.
M’ngono wanga amacedwa kugona.Ndimauka m’mamawa cifukwa ndine wa ngwilo!
My little brother sleeps
very late.
I wake early, because I
am great!
Ndine ndimatsegulako kuti dzuwa lilowe
I am the one who lets in
the sun.
”Ndiwe nthanda yanga,” amatelo amai kundiwuza.
“You’re my morning
star,” says Ma.
Ndimadzisamba ndekha matsiku onse, sindifunanso thandidzo ai.
I wash myself, I don’t
need any help.
Sindimaganiza zakuti madzi ndiyodzidzila, kapena sopo wa kamtambo wocapila dzobvala.
I can cope with cold
water and blue smelly
soap.
Amai amandikumbutsa kuti “osayiwala kutsuka mano”Ndimawayanka kuti “ine ai, sindingaiwale ai!”
Ma reminds, “Don’t
forget teeth.”
I reply, “Never, not
me!”
Ndikamalidza kusamba, ndimapatsa moni agogo amuna ndi alongo awo atate anga.Ndimawafunila tsiku labwino.
After washing, I greet
Grandpa and Auntie,
and wish them a good
day.
Ndipo ndimabvala ndekha.”Ndine wamkulu tsopano amama,” ndimawaudza.
Then I dress myself,
“I’m big now Ma,” I say.
Ndimanga mabatani komanso nthambo za nsapato ndekha.
I can close my buttons
and buckle my shoes.
Ndimayesetsa kuti mbale wanga adziwe nkhani zonse za kusukulu.
And I make sure little
brother knows all the
school news.
Ndimacita zonse zothekela munjira mukalasi.
In class I do my best in
every way.
Ndimacita zabwino zonsezi tsiku ndi tsiku.Koma ndimakondetsetsa kusowela kwambili!
I do all these good
things every day.
But the thing I like
most, is to play and
play!
Written by: Michael Oguttu
Illustrated by: Vusi Malindi
Translated by: Jessy Sakala