Anyamata anapepesa ponena Vusi. “Sitingathandizile pa nkhani ya keke, koma tenga kumtengo aka koyendela ukapatse mlongo wako,” umodzi mwa iwo anatelo. Vusi anapitiliza ndi ulendo wake.
Omanga nyumba anapepesa pothyola kamtengo. “Sitingathandizile pa nkhani ya keke, koma tenga mtolo wa udzu ukapatse mlongo wako,” umodzi pa omanga anatelo. Vusi anapitiliza ndi ulendo wake.
Ng’ombe inapepesa pokudya mtolo. Mlimi anamupatsa ng’ombe kukhala mphatso ya mlongo wa Vusi. Vusi anapiliza ulendo wake.
奶牛很抱歉,因为它太自私了。农民决定让奶牛跟着福思,作为礼物送给他姐姐。福思继续上路了。
Koma ng’ombe inathawila kumwine wake pa cakudya ca m’madzulo. Vusi anasowa paulendo wake. Anafika mocedwa kwambili pacikwati ca mlongo wake. Alendo anayamba kale kudya pacikwati.
但是,到了吃晚饭的时候,奶牛跑回农场了,福思也迷路了。他很晚才到姐姐的婚礼上,客人们已经在吃饭了。
“Kodi ndidzacita ciani?” Vusi analila. Ngo’mbe imene yathawa inali mphatso, m’malo mwa mtolo wa udzu umene anandipatsa omanga manyumba. Anthu omanga manyumba anandipatsa cifukwa anathyola kamtengo kamene anandipatsa othyola zipatso. Othyola zipatso anandipatsa kamtengo cifukwa anaphanya dzila la keke la mlongo wanga. Keke inali ya cikwati ca mlongo wanga. Tsopano kulibe dzila, kulibe keke, ndiponso kulibe mphatso.