Pomwe anakumana, Magozwe anayamba kuuza Thomas, nkhani za umoyo wake. Anamuuza za mwamene anathawila kucoka kwa amalume ake. Thomas sanakambe zambili, ndipo sanauze Magozwe zocita koma anamvetsela mwacidwi. Nthawi zina Magozwe ndi Thomas anakambilana pamene anali kudya munyumba ya tsindwi yamtambo.
Pomwe Magozwe anali pafupi ndikukwanitsa zaka khumi, Thomas anamupatsa buku. Buku inali pa za mnyamata wa m’mudzi amene anakula kukhala womenya bola odziwika kwambili. Thomas anamuwelengela Magozwe kambili, mpaka tsiku lina anakamba nati, “Niganiza kuti uyambe kupita ku sukulu, kuti ukaphunzile kuwelenga. Uganizapo bwanji?” Thomas ananena kuti anali kudziwa malo kumene ana angapite kukhala ndiponso kuphunzila kwameneko.
Anamuuza Thomas kuti anali ndi mantha. Thomas anamusimikidzila kuti, azakhala ndi umoyo wabwina kumalo atsopanowa.
他把自己的想法告诉了托马斯。托马斯对他循循善诱,终于说服了玛格威,他在新地方一定会过上更好的生活。
Motelo Magozwe anapita kukhala mu cipinda mu nyumba ya tsindwi yamsipu. Anakhala ndi anyamata ena awili mu cipinda. Pamodzi onse anali anyamata khumi amene anali kukhala panyumba paja. Pamodzi ndi a Anti Cissy ndi amuna ao, agalu atatu, cona ndi mbuzi yokalamba.
Magozwe anayamba sukulu ndipo cinali cobvuta. Ndizambili zimene anali kufunikila kudziwa kuti alingane ndi anzake. Nthawi zina anali kufuna kuleka. Koma anaganizila oyendetsa ndeke ndi omenya bola a mu mabuku ake anthano. Monga iwo anyamata a mu mabuku, sanaleke.
Magozwe anali khale panja panyumba ya tsindwi ya msipu, akuwelenga buku lake lakusukulu, Thomas anabwela ndi kukhala pafupi naye. “Ikamba ciani nkhani uwelenga?” anafunsa Thomas. “Ikamba pa za mnyamata amene anakhala mphunzitsi,” anayankha Magozwe. “Ndani dzina munyamata?” anafunsa Thomas. “Dzina lake ndi Magozwe,” anayankha Magozwe momwetula.