Udongo na Apiyo anali kunkala mu tauni na atate awo. Anali kukonda ntawi yamene masikulu anali ovala, cifukwa anali kuyenda pacuti kwa ambuya awo. Ambuya awo anali kunkala mu muzi wa pafupi na musinje waukulu.
Panapita ntawi ndipo ana awa anagona cifukwa analema.
过了一会儿,孩子们累了,就在车里睡着了。
Pamene anafika pa munzi, atate a Odongo na Apiyo ana usa ana. Ana anapeza ambuya awo aligone pa mpasa munsi mwa mutengo. Ambuya awo anali muzimai wampamvu, ndipo wokongola kwambili.
Siku lina ana anayenda ku musika na ambuya awo. Anayenda kukagulisa ndiyo za mumunda, shuga na sopo. Apiyo anali kukonda kuuza antu mitengo za vintu. Odongo anali kukonda kulongeza vintu vamena antu anali kugula.
Odongo na Apiyo sibanafune kubwelela ku tauni. Ana anapempa ambuya awo kuti ayende nawo ku tauni. Koma ambuya anati “Ndine nkalamba ndipo siningankale mu tauni, koma mukabwela kuno kumuzi muzakanipeza.”
Pamene Odongo na Apiyo anabwelele ku sukulu, anauza anzao za umoyo wakumunzi. Anzao ena anakonda umoyo wamu tauni koma ena anakonda umoyo wakumunzi. Koma onse ana ananena kuti ambuya a Odongo na Apiyo ni abwino mutima.