其他语言
中文
阿拉伯语
阿姆哈拉语
波兰语
波斯语
波斯语(阿富汗)
德语
俄语
法语
菲律宾语
韩语
孟加拉语
挪威语(书面)
挪威语(新)
旁遮普语
葡萄牙语
日语
斯瓦希里语
索马里语
土耳其语
乌尔都语
乌克兰语
西班牙语
意大利语
英语
粤语
越南语
藏语
更多语言…
返回故事列表
Kubwezela kwa Olozela kuli njuci
指蜜鸟的复仇
Zulu folktale
Wiehan de Jager
Sitwe Benson Mkandawire
Christine Mwanza
本故事尚未有语音版。
Iyi ndi nkhani ya Ngede, Olozela kuli njuci, ndi munyamata ozikonda ochedwa Gingire. Tsiku lina pamene Gingire anacokapo kukasaka nyama mthengo, anamva Ngede kuitana. Gingire anamva njala ya uci kwambili. Anaimilila ndikumvetsetsa, kusakila mpaka anaona kambalame m’mwamba mwamtengo. “Chiti-chiti-chiti,” mbalame inalila pamene inali kuulukila ku kumtengo wina ndi winanso. “Chiti-chiti-chiti,” kambalame kanaitana, ndikuimilila kawilikawili kutsimikizila kuti Gingire akubwela.
这是一个关于指蜜鸟奈吉和贪婪的年轻人青其儿的故事。有一天,青其儿外出打猎,忽然,他听到了奈吉的叫声。青其儿一想到跟着指蜜鸟就能找到美味的蜂蜜,口水就忍不住流了出来。他停下来,仔细地听着,四处找寻,直到他在头上的树枝里看到了指蜜鸟。小鸟啾啾啾地叫着,从一根树枝飞到另一个树枝。指蜜鸟一边飞一边叫,让青其儿能跟上它。
Patapita theka la ola limodzi, anafika pa m’tengo ukulu ochedwa mkuyu. Ngede analumphalumpha mu m’tengo. Anaima pa nthambi ina nagunduzila mutu wake kwa Gingire monga kumuuza kuti, “Zafika zili pano! Bwela tsopano. Cifukwa ciani ukucedwa?” Gingire sanaone njuci pansi pa mtengo koma anadalila Ngede.
过了大概半个小时,他们到了一棵巨大的野无花果树下。奈吉在树枝间跳来跳去,然后在其中一根树枝上停了下来,它朝青其儿伸出脑袋,好像在说:“就是这儿!快来!别磨磨蹭蹭的。”青其儿站在树下,看不到一只蜜蜂,但是他相信奈吉不会骗他。
Gingire anaika pansi mkondo wake munsi mwa mtengo, anatenga nkhuni nakuyatsa moto. Pamene moto unayaka bwino, anaika kamtengo katali pakati pamoto. Kamtengo kameneka kanali kuziwika pankhani yopanga utsi wambili pakuphya. Anayamba kukwela cimtengo ndi kamtengo ka utsi atagwila ndi mano.
青其儿把他打猎的矛搁在树下,搜集了一些干枯的小树枝,点了一堆火。当火慢慢旺起来的时候,他拿了一根又长又干的树枝,伸向火堆中心。这种木头烧起来的时候,会释放出很多烟。青其儿一手拿着树枝的另一头,另一只手抓着树干,开始爬树。
Posacedwa, anamva kulila kwa njuci. Zinali kulowa ndi kutuluka m’mphako. Pamene Gingire anafika, anaika kamtengo kautsi m’mphako. Njuci zinacoka mofulumila ndikukalipa. Zinathawa cifukwa sizinakonde utsi ndiponso zikalibe kupita, zinamuluma Gingire mwankhawa bii!
不久青其儿就听到了蜜蜂飞来飞去的嗡嗡声。它们在树干里筑了一个巢,正忙着飞进去飞出来。当青其儿爬到蜂巢附近的时候,他把树枝燃烧的一端猛地戳到蜂巢里。蜜蜂们害怕灰烟,它们都吓坏了,赶紧全都飞出来,但它们没忘记给青其儿脸上、身上狠狠地叮上几口。
Pamene njuci zinacoka, Gingire analowetsa manja ake mu m’mphako nacotsa uci wamadzimadzi odzala ndi mafuta oyela. Anaika uci wake mosamala mukacola kamene ananyamula paphewa, ndipo iye anayamba kutsika m’mtengo.
蜜蜂全都飞出来了,青其儿把手伸进蜂巢里,他挖到了好多蜜块,又甜又香的蜂蜜从蜜块上滴下来,看起来美味极了。他小心翼翼地把蜂蜜块放进肩膀上的袋子里,慢慢地从树上爬下来。
Ngede anali kuyangana zonse zimene Gingire anali kucita. Anali kuyembekeza kuti amusiyileko uci kuthokoza pomudziwitsa. Ngede anayesa kufendela pafupi kuti amuoneko. Gingire anafika pansi pa mtengo ndiponse Ngede anapalasulila pa mwala pafupi ndi mnyamata kuyembekezela kuti amupatseko.
奈吉迫不及待地看着青其儿做这些事情,它等着青其儿能送它一小块蜂蜜,作为给他引路的谢礼。青其儿在树枝间轻快地跳来跳去,离地面越来越近。终于青其儿稳稳地落地,奈吉落在他附近的一块石头上,等着青其儿给他的礼物。
Koma Gingire anazima moto, ndi kunyamula mkondo wake ndikupita kunyumba osakumbuka Ngede. Ngede anamuitana mokalipa, “VIC-toll! VIC-tolll!” Gingire anaimilila, anayangana kambalame ndi kuseka kwambili. “Ufuna uci, ha mzanga? Ndasewenza ndi kulumidwa ndekha! Ndicifukwa ciani ufuna ndikupatseko uci wabwino tele?” Iye anapita. Ngede anakalipa kwambili! Sanayenele kumucita motele! Koma azabwezela tsiku lina.
但是青其儿把火灭了,拎起他的矛,开始向家里走去,装作看不见奈吉的样子。奈吉生气地叫着:“给我蜂蜜!给我蜂蜜!”青其儿停下来,盯着小鸟,大笑说:“我的朋友,你也想要蜂蜜,是吗?哈哈,我做了这么多事,被叮了那么多包!我为什么要跟你分享这蜂蜜?”说完,青其儿就走远了。奈吉气极了,他可从来没有被这样对待过!等着吧,它会报仇的。
Tsiku lina masabata atapitapo, Gingire anamvelanso kuitana kwa uci kwa Ngede. Anakumbukila uci wabwino uja ndiponso iye anakalondolanso kambalameko. Pamene Gingire analondola kambalane, kanamupeleka kumathelo kwa thengo, Ngede anaimilila kuti apumuleko mcimtengo ca minga. “Ahh,” anaganiza Gingire. “Mphako ya njuci ifunikila kupezeka m’mtengowu.” Anayatsa moto mwamsanga nakuyamba kukwela, ndikamtengo ka utsi kukamwa. Ngede anakhala cete ndi kupenyelela.
过了几个星期,青其儿又听到了奈吉的叫声。他想起来美味的蜂蜜,迫不及待地跟着指蜜鸟走了。奈吉领着青其儿走到森林边上,在一棵大树冠上停了下来。青其儿心想:“哈哈,树上肯定有蜂巢。”他迅速地生了一小堆火,拿着燃烧的树枝开始爬树。奈吉停在那儿看着这一切。
Gingire anakwela, ndikudabwa cifukwa ciani sakumvela njuci monga mwanthawi zonse. “Kapena mphako ya njuci ili mkati kwambili mwa mtengo,” anaziganizila. Anasendelelako pamwamba pa nthambi ina. Koma m’malo mwakuona mphako, anaonana ndi nyalugwe! Nyalungwe anakalipa kwambili pomusokoneza tulo twake. Nyalugwe anakalipa pomusokonezela tulo twake. Anacepetsa maso ake, ndikutsegula kamwa kake kuonetsa mano ake akulu akuthwa.
青其儿爬着爬着,心里觉得奇怪,怎么他没有听到嗡嗡声呢?他想,蜂巢一定在树冠很深的地方。他拉着树枝,跳上树:没有蜂巢,他看到了一只豹子!豹子非常生气,因为青其儿打扰了它的美梦。豹子眯着眼睛,张开血盆大口,露出了又白又尖的牙齿。
Pamene Nyalungwe akalibe kumuluma Gingire, anaseluka cimtengo mwamsanga. Mofulumila anaphonya nthambi, anagwa kuipa kucoka m’mtengo nakuzicita mwendo. Anathawa mwamsanga kuyopa nyalugwe. Mwamwai, Nyalugwe anali natulo kwambili ndiponso iye sanamuthamangitse. Ngede, olozela njuci anabwezela. Ndiponso Gingire anaphunzililapo.
青其儿没等到豹子扑向他,就飞快地爬下树。可他爬得太匆忙了,一脚没踩稳,重重地摔在地上,扭到了脚踝。他一瘸一拐地跑走了。幸好豹子还没睡醒,没有追青其儿。指蜜鸟奈吉报了仇,青其儿也学到了教训。
Ngati ana aGingire amvela nkhani ya Ngede, amakapatsa ulemu kanyoni. Akacosa uci, amasiyako uci wambili kuti olozela njuci adye!
从此以后,青其儿的孩子们都听说了奈吉的故事,都非常尊重这只小鸟。他们每次收获蜂蜜的时候,都会把最大的一块留给指蜜鸟。
作者: Zulu folktale
插图: Wiehan de Jager
译文: Sitwe Benson Mkandawire
配音: Christine Mwanza